Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 0:54

[1] Tamandani Yehova. Tamandani Mulungu mʼmalo ake opatulika; mutamandeni ku thambo lake lamphamvu.

[2] Mutamandeni chifukwa cha machitidwe ake amphamvu; mutamandeni chifukwa cha ukulu wake wopambana.

[3] Mutamandeni poyimba malipenga, mutamandeni ndi pangwe ndi zeze.

[4] Mutamandeni ndi matambolini ndi kuvina, mutamandeni ndi zingwe ndi zitoliro.

[5] Mutamandeni ndi ziwaya zolira za malipenga, mutamandeni ndi ziwaya zolira kwambiri.

[6] Chamoyo chilichonse chopuma chitamande Yehova. Tamandani Yehova.

Masalimo — Chapters