[1] Tamanda Yehova, iwe moyo wanga; ndi zonse zamʼkati mwanga zitamande dzina lake loyera.
[2] Tamanda Yehova, iwe moyo wanga, ndipo usayiwale zabwino zake zonse.
[3] Amene amakhululuka machimo ako onse ndi kuchiritsa nthenda zako zonse,
[4] amene awombola moyo wako ku dzenje ndi kukuveka chikondi ndi chifundo chake ngati chipewa chaufumu,
[5] amene akwaniritsa zokhumba zako ndi zinthu zabwino, kotero kuti umakhala wamphamvu zatsopano ngati mphungu.
[6] Yehova amachita chilungamo ndipo amaweruza molungama onse opsinjika.
[7] Iye anadziwitsa Mose njira zake, ntchito zake kwa Aisraeli.
[8] Yehova ndi wachifundo ndi wokoma mtima, wosakwiya msanga ndi wachikondi chochuluka.
[9] Iye sadzatsutsa nthawi zonse, kapena kusunga mkwiyo wake kwamuyaya;
[10] satichitira molingana ndi machimo athu, kapena kutibwezera molingana ndi mphulupulu zathu.
[11] Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, koteronso chikondi chake nʼchachikulu kwa iwo amene amamuopa;
[12] monga kummawa kutalikirana ndi kumadzulo, koteronso Iye watichotsera mphulupulu zathu kuti zikhale kutali nafe.
[13] Monga bambo amachitira chifundo ana ake, choncho Yehova ali ndi chifundo ndi iwo amene amamuopa;
[14] pakuti Iye amadziwa momwe tinawumbidwira, amakumbukira kuti ndife fumbi.
[15] Kunena za munthu, masiku ake ali ngati udzu, amaphuka ngati duwa la mʼmunda;
[16] koma mphepo imawombapo ndipo silionekanso ndipo malo ake sakumbukirikanso.
[17] Koma kuchokera muyaya mpaka muyaya chikondi cha Yehova chili ndi iwo amene amamuopa, ndi chilungamo chake chili ndi ana a ana awo;
[18] iwo amene amasunga pangano lake ndi kukumbukira kumvera malangizo ake.
[19] Yehova wakhazikitsa mpando wake waufumu mmwamba ndipo ufumu wake umalamulira onse.
[20] Tamandani Yehova, inu angelo ake, amphamvu inu amene mumachita zimene amalamula, amene mumamvera mawu ake.
[21] Tamandani Yehova, zolengedwa zonse zakumwamba, inu atumiki ake amene mumachita chifuniro chake.
[22] Tamandani Yehova, ntchito yake yonse kulikonse mu ulamuliro wake. Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.