Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:29

[1] Wamphamvuyo, Yehova Mulungu, akuyankhula ndi kuyitanitsa dziko lapansi kuyambira kotulukira dzuwa mpaka kumene limalowera.

[2] Kuchokera ku Ziyoni, mokongola kwambiri Mulungu akuwala.

[3] Mulungu wathu akubwera ndipo sadzakhala chete; moto ukunyeketsa patsogolo pake, ndipo pomuzungulira pali mphepo yamkuntho

[4] Iye akuyitanitsa zamumlengalenga ndi za pa dziko lapansi kuti aweruze anthu ake.

[5] Mundisonkhanitsire okhulupirika anga, amene anachita pangano ndi ine pochita nsembe.

[6] Ndipo mayiko akumwamba akulengeza chilungamo chake, pakuti Mulungu mwini ndi woweruza.

[7] Imvani inu anthu anga, ndipo Ine ndidzayankhula, iwe Israeli, ndipo Ine ndidzayankhula mokutsutsa; ndine Mulungu, Mulungu wako.

[8] Sindikudzudzula chifukwa cha nsembe zako, kapena nsembe zako zopsereza zimene zili pamaso panga nthawi zonse.

[9] Ine sindikufuna ngʼombe yayimuna kuchokera mʼkhola lako kapena mbuzi za mʼkhola lako,

[10] pakuti nyama iliyonse yakunkhalango ndi yanga ndiponso ngʼombe za ku mapiri ochuluka.

[11] Ine ndimadziwa mbalame iliyonse mʼmapiri ndiponso zolengedwa zonse zakutchire ndi zanga.

[12] Ndikanakhala ndi njala sindikanakuwuzani, pakuti dziko lonse ndi zonse zimene zili mʼmenemo ndi zanga.

[13] Kodi ndimadya nyama ya ngʼombe zazimuna kapena kumwa magazi a mbuzi?

[14] “Pereka nsembe zachiyamiko kwa Mulungu, kwaniritsa malonjezo ako kwa Wammwambamwamba.

[15] Ndipo undiyitane pa tsiku lako la masautso; Ine ndidzakulanditsa, ndipo udzandilemekeza.”

[16] Koma kwa woyipa, Mulungu akuti, “Kodi uli ndi mphamvu yanji kuti uzinena malamulo anga kapena kutenga pangano langa pa milomo yako?

[17] Iwe umadana ndi malangizo anga ndipo umaponyera kumbuyo kwako mawu anga.

[18] Ukaona wakuba umamutsatira, umachita maere ako pamodzi ndi achigololo

[19] Umagwiritsa ntchito pakamwa pako pa zinthu zoyipa ndipo umakonza lilime lako kuchita chinyengo.

[20] Nthawi zonse umayankhula motsutsana ndi mʼbale wako ndipo umasinjirira mwana wa amayi ako enieni.

[21] Wachita zimenezi ndipo Ine ndinali chete; umaganiza kuti ndine wofanana nawe koma ndidzakudzudzula ndipo ndidzakutsutsa pamaso pako.

[22] “Ganizira izi, iwe amene umayiwala Mulungu kuti ndingakukadzule popanda wokupulumutsa:

[23] Iye amene amapereka nsembe yamayamiko amandilemekeza, ndipo amakonza njira zake kuti ndimuonetse chipulumutso cha Mulungu.”

Masalimo — Chapters