[1] Malo anu okhalamo ndi okomadi, Inu Yehova Wamphamvuzonse!
[2] Moyo wanga ukulakalaka, mpaka kukomoka, kufuna mabwalo a Yehova; Mtima wanga ndi thupi langa zikufuwulira Mulungu wamoyo.
[3] Ngakhale timba wapeza nyumba yokhalamo, ndiponso namzeze wadzipezera yekha chisa, kumene amagonekako ana ake pafupi ndi guwa lanu la nsembe, Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga.
[4] Odala amene amakhala mʼNyumba yanu; nthawi zonse amakutamandani. q4 Sela
[5] Odala amene mphamvu yawo ili mwa Inu, mitima yawo ikufunitsitsa kuyenda mʼmisewu yopita ku Ziyoni.
[6] Pamene akudutsa chigwa cha Baka, amachisandutsa malo a akasupe; mvula ya chizimalupsa imadzazanso mayiwe ake.
[7] Iwo amanka nakulirakulira mphamvu mpaka aliyense ataonekera pamaso pa Mulungu mu Ziyoni.
[8] Imvani pemphero langa, Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse; mvereni Inu Mulungu wa Yakobo. q4 Sela
[9] Yangʼanani chishango chathu, Inu Mulungu; yangʼanani mokoma mtima pa wodzozedwa wanu.
[10] Nʼkwabwino kukhala mʼmabwalo anu tsiku limodzi kuposa kukhala kwina kwake kwa zaka 1,000; Ine ndingakonde kukhala mlonda wa pa khomo la Nyumba ya Mulungu wanga kuposa kukhala mʼmatenti a anthu oyipa.
[11] Pakuti Yehova Mulungu ndi dzuwa ndi chishango; Yehova amapereka chisomo ndi ulemu; Iye sawamana zinthu zabwino iwo amene amayenda mwangwiro.
[12] Inu Yehova Wamphamvuzonse, wodala ndi munthu amene amakhulupirira Inu.