Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:04

[1] Yehova imvani pemphero langa, mvetserani kulira kwanga kopempha chifundo; mwa kukhulupirika kwanu ndi chilungamo chanu bwerani kudzandithandiza.

[2] Musazenge mlandu mtumiki wanu, pakuti palibe munthu wamoyo amene ndi wolungama pamaso panu.

[3] Mdani akundithamangitsa, iye wandipondereza pansi; wachititsa kuti ndikhale mu mdima ngati munthu amene anafa kale.

[4] Choncho mzimu wanga ukufowoka mʼkati mwanga; mʼkati mwanga, mtima wanga uli ndi nkhawa.

[5] Ndimakumbukira masiku amakedzana; ndimalingalira za ntchito yanu yonse, ndimaganizira zimene manja anu anachita.

[6] Ndatambalitsa manja anga kwa Inu; moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Inu monga nthaka yowuma. q4 Sela

[7] Yehova ndiyankheni msanga; mzimu wanga ukufowoka. Musandibisire nkhope yanu, mwina ndidzakhala ngati iwo amene atsikira ku dzenje.

[8] Lolani kuti mmawa ubweretse mawu achikondi chanu chosasinthika, pakuti ine ndimadalira Inu. Mundisonyeze njira yoti ndiyendemo, pakuti kwa Inu nditukulira moyo wanga.

[9] Pulumutseni kwa adani anga, Inu Yehova, pakuti ndimabisala mwa Inu.

[10] Phunzitseni kuchita chifuniro chanu, popeza ndinu Mulungu wanga; Mzimu wanu wabwino unditsogolere pa njira yanu yosalala.

[11] Sungani moyo wanga Inu Yehova chifukwa cha dzina lanu; mwa chilungamo chanu tulutseni mʼmasautso anga.

[12] Mwa chikondi chanu chosasinthika khalitsani chete adani anga; wonongani adani anga, pakuti ndine mtumiki wanu.

Masalimo — Chapters