Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:23

[1] Tcherani khutu ku mawu anga, Inu Yehova, ganizirani za kusisima kwanga

[2] Mverani kulira kwanga kofuna thandizo, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga, pakuti kwa Inu, ine ndikupemphera.

[3] Mmawa, Yehova mumamva mawu anga; Mmawa ndimayala zopempha zanga pamaso panu ndi kudikira mwachiyembekezo.

[4] Inu si Mulungu amene mumasangalala ndi zoyipa; choyipa sichikhala pamaso panu.

[5] Onyada sangathe kuyima pamaso panu; Inu mumadana ndi onse ochita zoyipa.

[6] Mumawononga iwo amene amanena mabodza; anthu akupha ndi achinyengo, Yehova amanyansidwa nawo.

[7] Koma Ine, mwa chifundo chanu chachikulu, ndidzalowa mʼNyumba yanu; mwa ulemu ndidzaweramira pansi kuyangʼana ku Nyumba yanu yoyera.

[8] Tsogolereni Inu Yehova, mwa chilungamo chanu chifukwa cha adani anga ndipo wongolani njira yanu pamaso panga.

[9] Palibe mawu ochokera mʼkamwa mwawo amene angadalirike; mtima wawo wadzaza ndi chiwonongeko. Kummero kwawo kuli ngati manda apululu; ndi lilime lawo amayankhula zachinyengo.

[10] Lengezani kuti ndi olakwa, Inu Mulungu! Zochita zawo zoyipa zikhale kugwa kwawo. Achotseni pamaso panu chifukwa cha machimo awo ambiri, pakuti awukira Inu.

[11] Koma lolani kuti onse amene apeza chitetezo mwa Inu akondwere; lolani kuti aziyimba nthawi zonse chifukwa cha chimwemwe. Aphimbeni ndi chitetezo chanu, iwo amene amakonda dzina lanu akondwere mwa Inu.

[12] Ndithu, Inu Yehova, mumadalitsa olungama; mumawazungulira ndi kukoma mtima kwanu ngati chishango.

Masalimo — Chapters