Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:05

[1] Imbirani Yehova nyimbo yatsopano; Imbirani Yehova dziko lonse lapansi.

[2] Imbirani Yehova, tamandani dzina lake; lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.

[3] Lengezani ulemerero wake pakati pa mayiko, ntchito zake zodabwitsa pakati pa mitundu yonse ya anthu.

[4] Pakuti wamkulu ndi Yehova ndipo ndi woyenera kwambiri kumutamanda; ayenera kuopedwa kupambana milungu yonse.

[5] Pakuti milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi mafano, koma Yehova analenga mayiko akumwamba.

[6] Ulemu ndi ufumu zili pamaso pake, mphamvu ndi ulemerero zili mʼmalo ake opatulika.

[7] Perekani kwa Yehova, inu mabanja a anthu a mitundu ina, perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu.

[8] Perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake; bweretsani chopereka ndipo mulowe mʼmabwalo ake.

[9] Lambirani Yehova mu ulemerero wa chiyero chake; njenjemerani pamaso pake, dziko lonse lapansi.

[10] Nenani pakati pa mitundu ya anthu, “Yehova akulamulira.” Dziko lonse lakhazikika molimba, silingasunthidwe; Iye adzaweruza mitundu ya anthu molungama.

[11] Mayiko akumwamba asangalale, dziko lapansi likondwere; nyanja ikokome, ndi zonse zili mʼmenemo;

[12] minda ikondwere pamodzi ndi chilichonse chili mʼmenemo. Pamenepo mitengo yonse ya mʼnkhalango idzayimba ndi chimwemwe;

[13] idzayimba pamaso pa Yehova, pakuti Iye akubwera kudzaweruza dziko lapansi; adzaweruza dziko lonse mwachilungamo ndi mitundu ya anthu onse mʼchoonadi.

Masalimo — Chapters