Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:52

[1] Yehova akulamulira, dziko lapansi lisangalale; magombe akutali akondwere.

[2] Mitambo ndi mdima waukulu zamuzungulira; chilungamo ndi kuweruza molungama ndiwo maziko a mpando wake waufumu.

[3] Moto umapita patsogolo pake ndi kunyeketsa amaliwongo kumbali zonse.

[4] Zingʼaningʼani zake zimawalitsa dziko lonse; dziko lapansi limaona ndipo limanjenjemera.

[5] Mapiri amasungunuka ngati phula pamaso pa Yehova, pamaso pa Ambuye a dziko lonse lapansi.

[6] Mayiko akumwamba amalengeza za chilungamo chake, ndipo mitundu yonse ya anthu imaona ulemerero wake.

[7] Onse amene amalambira mafano osema amachititsidwa manyazi, iwo amene amanyadira mafano; mulambireni, inu milungu yonse!

[8] Ziyoni akumva ndipo akukondwera, midzi ya Yuda ikusangalala chifukwa cha maweruzo anu Yehova.

[9] Pakuti Inu Yehova ndi Wammwambamwamba pa dziko lonse lapansi; ndinu wokwezeka kupambana milungu yonse.

[10] Iwo amene amakonda Yehova adane ndi zoyipa pakuti Iye amayangʼanira miyoyo ya amene amamukhulupirira ndipo amawapulumutsa mʼdzanja la anthu oyipa

[11] Kuwala kumafika pa anthu olungama, ndi chimwemwe kwa olungama mtima.

[12] Kondwerani mwa Yehova Inu olungama ndipo tamandani dzina lake loyera.

Masalimo — Chapters