Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 20:01

[1] Odala ndi amene moyo wawo ulibe cholakwa, amene amayenda monga mwa malamulo a Yehova.

[2] Odala ndi amene amasunga malamulo ake, amene amafunafuna Iyeyo ndi mtima wawo wonse.

[3] Sachita cholakwa chilichonse; amayenda mʼnjira zake.

[4] Inu mwapereka malangizo ndipo ayenera kutsatidwa kwathunthu.

[5] Aa! Ndikanakonda njira zanga zikanakhala zokhazikika pa kumvera zophunzitsa zanu!

[6] Pamenepo ine sindikanachititsidwa manyazi, poganizira malamulo anu onse.

[7] Ndidzakutamandani ndi mtima wolungama, pamene ndikuphunzira malamulo anu olungama.

[8] Ndidzamvera zophunzitsa zanu; musanditaye kwathunthu. Beti

[9] Kodi mnyamata angathe bwanji kuyeretsa mayendedwe ake? Akawasamala potsata mawu anu.

[10] Ndimakufunafunani ndi mtima wanga wonse; musalole kuti ndisochere kuchoka pa malamulo anu.

[11] Ndasunga mawu anu mu mtima mwanga kuti ndisakuchimwireni.

[12] Mutamandike Inu Yehova; phunzitseni malamulo anu.

[13] Ndi milomo yanga ndimafotokoza malamulo anu onse amene amachokera pakamwa panu.

[14] Ndimakondwera potsatira malamulo anu monga momwe munthu amakondwera akakhala ndi chuma chambiri.

[15] Ndimalingalira malangizo anu ndipo ndimaganizira njira zanu.

[16] Ndimakondwera ndi malamulo anu; sindidzayiwala konse mawu anu. Gimeli

[17] Chitirani zokoma mtumiki wanu, ndipo ndidzakhala ndi moyo; kuti tsono ndisunge mawu anu.

[18] Tsekulani maso anga kuti ndithe kuona zinthu zodabwitsa mʼmalamulo anu.

[19] Ine ndine mlendo pa dziko lapansi; musandibisire malamulo anu.

[20] Moyo wanga wafowoka polakalaka malamulo anu nthawi zonse.

[21] Inu mumadzudzula onyada, otembereredwa, amene achoka pa malamulo anu.

[22] Mundichotsere chitonzo ndi mnyozo pakuti ndimasunga malamulo anu.

[23] Ngakhale mafumu akhale pamodzi kundinyoza, mtumiki wanu adzalingalirabe zophunzitsa zanu.

[24] Malamulo anu amandikondweretsa; ndiwo amene amandilangiza. Daleti

[25] Moyo wanga wakangamira fumbi; tsitsimutseni molingana ndi mawu anu.

[26] Ndinafotokoza njira zanga ndipo Inu munandiyankha; phunzitseni malamulo anu.

[27] Mundidziwitse chiphunzitso cha malangizo anu; pamenepo ndidzalingalira zodabwitsa zanu.

[28] Moyo wanga wafowoka ndi chisoni; limbikitseni monga mwa mawu anu.

[29] Mundichotse mʼnjira zachinyengo; mundikomere mtima pondiphunzitsa malamulo anu.

[30] Ndasankha njira ya choonadi; ndayika malamulo anu pa mtima panga.

[31] Ndagwiritsitsa umboni wanu, Inu Yehova; musalole kuti ndichititsidwe manyazi.

[32] Ndimathamanga mʼnjira ya malamulo anu, pakuti Inu mwamasula mtima wanga. He

[33] Yehova, phunzitseni kutsatira zophunzitsa zanu; ndipo ndidzazisunga mpaka kumapeto.

[34] Mundipatse mtima womvetsa zinthu ndipo ndidzasunga malamulo anu ndi kuwamvera ndi mtima wanga wonse.

[35] Munditsogolere mʼnjira ya malamulo anu, pakuti mʼmenemo ndimapezamo chikondwerero changa.

[36] Tembenuzani mtima wanga kuti uzikonda malamulo anu, osati chuma.

[37] Tembenuzani maso anga kuchoka ku zinthu zachabechabe; sungani moyo wanga monga mwa mawu anu.

[38] Kwaniritsani lonjezo lanu kwa mtumiki wanu, kuti Inu muopedwe.

[39] Mundichotsere chipongwe chimene ndikuchiopa, pakuti malamulo anu ndi abwino.

[40] Taonani, ndimalakalakatu malangizo anu! Sungani moyo wanga mʼchilungamo chanu. Wawi

[41] Chikondi chanu chosasinthika chibwere kwa ine, Inu Yehova, chipulumutso chanu monga mwa lonjezo lanu;

[42] ndipo ndidzayankha amene amandinyoza, popeza ndimadalira mawu anu.

[43] Musakwatule mawu a choonadi mʼkamwa mwanga, pakuti ndakhazikitsa chiyembekezo changa mʼmalamulo anu.

[44] Ndidzasunga malamulo anu nthawi zonse, ku nthawi za nthawi.

[45] Ndidzayendayenda mwaufulu, chifukwa ndinafunafuna malangizo anu.

[46] Ndidzayankhula za umboni wanu pamaso pa mfumu ndipo sindidzachititsidwa manyazi,

[47] popeza ndimakondwera ndi malamulo anu chifukwa ndimawakonda.

[48] Ndikweza manja anga ku malamulo anu, ku malamulo amene ndimawakonda, ndipo ndimalingalira malangizo anu. Zayini

[49] Kumbukirani mawu anu kwa mtumiki wanu, popeza mwandipatsa chiyembekezo.

[50] Chitonthozo changa pa masautso anga ndi ichi: lonjezo lanu limasunga moyo wanga.

[51] Odzikuza amandinyoza popanda chowaletsa, koma sindichoka pa malamulo anu.

[52] Ndimakumbukira malamulo anu Yehova akalekale, ndipo mwa iwo ndimapeza chitonthozo.

[53] Ndayipidwa kwambiri chifukwa cha oyipa amene ataya malamulo anu.

[54] Zophunzitsa zanu ndi mitu ya nyimbo yanga kulikonse kumene ndigonako.

[55] Usiku ndimakumbukira dzina lanu Yehova, ndipo ndidzasunga malamulo anu.

[56] Ichi ndicho ndakhala ndikuchita: ndimasunga malangizo anu. Heti

[57] Yehova, Inu ndiye gawo langa; ndalonjeza kumvera mawu anu.

[58] Ndimafunafuna nkhope yanu ndi mtima wanga wonse; mundikomere mtima monga mwa lonjezo lanu.

[59] Ndinalingalira za njira zanga ndipo ndatembenuza mayendedwe anga kutsatira umboni wanu.

[60] Ndidzafulumira ndipo sindidzazengereza kumvera malamulo anu.

[61] Ngakhale oyipa andimange ndi zingwe, sindidzayiwala lamulo lanu.

[62] Ndimadzuka pakati pa usiku kuyamika Inu chifukwa cha malamulo anu olungama.

[63] Ine ndine bwenzi la onse amene amakukondani, kwa onse amene amatsatira malangizo anu.

[64] Dziko lapansi ladzaza ndi chikondi chanu chosasinthika, phunzitseni malamulo anu. Teti

[65] Inu Yehova, chitirani chabwino mtumiki wanu molingana ndi mawu anu.

[66] Phunzitseni nzeru ndi chiweruzo chabwino, pakuti ndimakhulupirira malamulo anu.

[67] Ndisanayambe kuzunzika ndinasochera, koma tsopano ndimamvera mawu anu.

[68] Inu ndinu abwino ndipo zimene mumachita ndi zabwino; phunzitseni malamulo anu.

[69] Ngakhale odzikuza andipaka mabodza, ine ndimasunga malangizo anu ndi mtima wanga wonse.

[70] Mitima yawo ndi yowuma ndi yosakhudzidwa, koma ine ndimakondwera ndi malamulo anu.

[71] Ndi bwino kuti ndinasautsidwa kuti ndithe kuphunzira malamulo anu.

[72] Lamulo lochokera mʼkamwa mwanu limandikomera kwambiri kuposa ndalama zambirimbiri za siliva ndi golide. Yodi

[73] Manja anu anandilenga ndi kundiwumba; patseni nzeru zomvetsa zinthu kuti ndiphunzire malamulo anu.

[74] Iwo amene amakuopani akondwere akandiona, chifukwa chiyembekezo changa chili mʼmawu anu.

[75] Ine ndikudziwa, Inu Yehova, kuti malamulo anu ndi olungama ndipo mwandizunza chifukwa cha kukhulupirika kwanu.

[76] Chikondi chanu chosasinthika chikhale chitonthozo changa, molingana ndi lonjezo lanu kwa mtumiki wanu.

[77] Chifundo chanu chindifikire kuti ndikhale ndi moyo, popeza malamulo anu ndiye chikondwerero changa.

[78] Odzikuza achititsidwe manyazi chifukwa cha kundilakwira popanda chifukwa; koma ine ndidzalingalira malangizo anu.

[79] Iwo amene amakuopani atembenukire kwa ine, iwo amene amamvetsetsa umboni wanu.

[80] Mtima wanga ukhale wopanda cholakwa pa chiphunzitso chanu kuti ndisachititsidwe manyazi. Kafu

[81] Moyo wanga wafowoka ndi kufunafuna chipulumutso chanu, koma chiyembekezo changa chili mʼmawu anu.

[82] Maso anga alefuka pofunafuna lonjezo lanu; Ine ndikuti, “Kodi mudzanditonthoza liti?”

[83] Ngakhale ndili ngati thumba lachikopa la vinyo pa utsi sindiyiwala zophunzitsa zanu.

[84] Kodi mtumiki wanu ayenera kudikira mpaka liti? Kodi mudzawalanga liti amene amandizunza?

[85] Anthu osalabadira za Mulungu, odzikuza amandikumbira dzenje motsutsana ndi malamulo anu.

[86] Malamulo anu onse ndi odalirika; thandizeni, pakuti anthu akundizunza popanda chifukwa.

[87] Iwo anatsala pangʼono kundichotsa pa dziko lapansi koma sindinataye malangizo anu.

[88] Sungani moyo wanga molingana ndi chikondi chanu chosasinthika, ndipo ndidzamvera umboni wa pakamwa panu. Lamedi

[89] Mawu anu Yehova ndi amuyaya; akhazikika kumwambako.

[90] Kukhulupirika kwanu kumakhala mpaka ku mibado yonse; Inu munakhazikitsa dziko lapansi ndipo lilipobe.

[91] Malamulo anu alipobe mpaka lero lino, pakuti zinthu zonse zimatumikira Inu.

[92] Malamulo anu akanapanda kukhala chikondwerero changa, ndikanawonongeka mʼmasautso anga.

[93] Ine sindidzayiwala konse malangizo anu, pakuti ndi malangizo anuwo munasunga moyo wanga.

[94] Ndine wanu, ndipulumutseni; pakuti ndasamala malangizo anu.

[95] Anthu oyipa akudikira kuti andiwononge, koma ndidzalingalira umboni wanu.

[96] Ndadziwa kuti zinthu zonse zili ndi malire, koma malamulo anu alibe malire konse. Memu

[97] Ndithu, ine ndimakonda malamulo anu! Ndimalingaliramo tsiku lonse.

[98] Malamulo anu amachititsa kuti ndikhale wanzeru kuposa adani anga, popeza malamulowo ali ndi ine nthawi zonse.

[99] Ndimamvetsa zinthu kwambiri kuposa aphunzitsi anga onse popeza ndimalingalira umboni wanu.

[100] Ndili ndi nzeru zochuluka zomvetsera zinthu kuposa anthu okalamba, popeza ndimamvera malangizo anu.

[101] Ndimaletsa miyendo yanga kuyenda mʼnjira iliyonse yoyipa kuti ndithe kumvera mawu anu.

[102] Sindinapatuke kuchoka pa malamulo anu, pakuti Inu mwini munandiphunzitsa.

[103] Mawu anu ndi otsekemera ndikawalawa, otsekemera kuposa uchi mʼkamwa mwanga!

[104] Ndimapeza nzeru zodziwira zinthu kuchokera mʼmalangizo anu; kotero ndimadana ndi njira iliyonse yoyipa. Nuni

[105] Mawu anu ndi nyale ya kumapazi kwanga ndi kuwunika kwa pa njira yanga.

[106] Ndalumbira ndipo ndatsimikiza, kuti ndidzatsatira malamulo anu olungama.

[107] Ndazunzika kwambiri; Inu Yehova, sungani moyo wanga molingana ndi mawu anu.

[108] Inu Yehova, landirani matamando aufulu ochokera pakamwa panga, ndipo ndiphunzitseni malamulo anu.

[109] Ngakhale moyo wanga umakhala mʼzoopsa nthawi ndi nthawi, sindidzayiwala malamulo anu.

[110] Anthu oyipa anditchera msampha, koma sindinasochere kuchoka pa malangizo anu.

[111] Umboni wanu ndiye cholowa changa kwamuyaya; Iwo ndiye chimwemwe cha mtima wanga.

[112] Mtima wanga wakhazikika pa kusunga zophunzitsa zanu mpaka kumapeto kwenikweni. Samekhi

[113] Ndimadana ndi anthu apawiripawiri, koma ndimakonda malamulo anu.

[114] Inu ndinu pothawirapo panga ndi chishango changa; chiyembekezo changa chili mʼmawu anu.

[115] Chokani kwa ine, inu anthu ochita zoyipa, kuti ndisunge malamulo a Mulungu wanga!

[116] Mundichirikize molingana ndi lonjezo lanu, ndipo ndidzakhala ndi moyo; musalole kuti chiyembekezo changa chipite pachabe.

[117] Gwirizizeni, ndipo ndidzapulumutsidwa; nthawi zonse ndidzasamalira zophunzitsa zanu.

[118] Inu mumakana onse amene amasochera kuchoka pa zophunzitsa zanu, pakuti chinyengo chawo ndi chopanda phindu.

[119] Anthu onse oyipa a pa dziko lapansi mumawayesa ngati zinthu zakudzala; nʼchifukwa chake ndimakonda umboni wanu.

[120] Thupi langa limanjenjemera chifukwa cha kuopa Inu; ndimachita mantha ndi malamulo anu. Ayini

[121] Ndachita zolungama ndi zabwino; musandisiye mʼmanja mwa ondizunza.

[122] Onetsetsani kuti mtumiki wanu akukhala bwino, musalole kuti anthu odzikuza andipondereze.

[123] Maso anga alefuka, kufunafuna chipulumutso chanu, kufunafuna lonjezo lanu lolungama.

[124] Muchite naye mtumiki wanu molingana ndi chikondi chanu chosasinthika, ndipo mundiphunzitse malamulo anu.

[125] Ine ndine mtumiki wanu; patseni mzimu wondizindikiritsa, kuti ndimvetsetse umboni wanu.

[126] Yehova, ndi nthawi yoti muchitepo kanthu; malamulo anu akuswedwa.

[127] Chifukwa choti ndimakonda malamulo anu kuposa golide, kuposa golide woyengeka bwino,

[128] ndiponso chifukwa choti ndimaona kuti malangizo anu onse ndi wowongoka, ndimadana ndi njira iliyonse yoyipa. Pe

[129] Maumboni anu ndi odabwitsa nʼchifukwa chake ndimawamvera.

[130] Mawu anu akamaphunzitsidwa amapereka kuwunika; ngakhale anthu wamba amamvetsetsa.

[131] Ndimatsekula pakamwa panga ndi kupuma wefuwefu, kufunafuna malamulo anu.

[132] Tembenukirani kwa ine ndipo mundichitire chifundo, monga mumachitira nthawi zonse kwa iwo amene amakonda dzina lanu.

[133] Tsogolerani mayendedwe anga molingana ndi mawu anu; musalole kuti tchimo lizindilamulira.

[134] Ndiwomboleni mʼdzanja la anthu ondizunza, kuti ndithe kumvera malangizo anu.

[135] Nkhope yanu iwalire mtumiki wanu ndipo mundiphunzitse malamulo anu.

[136] Mitsinje ya misozi ikuyenda kuchoka mʼmaso mwanga, chifukwa anthu sakumvera malamulo anu. Tsade

[137] Yehova ndinu wolungama, ndipo malamulo anu ndi abwino.

[138] Maumboni amene munatipatsa ndi olungama; ndi odalirika ndithu.

[139] Ndikusautsidwa kwambiri mʼkati mwanga chifukwa adani anu amanyalanyaza mawu anu.

[140] Mawu anu ndi woyera kwambiri nʼchifukwa chake mtumiki wanune ndimawakonda.

[141] Ngakhale ndili wamngʼono ndi wonyozeka, sindiyiwala malangizo anu.

[142] Chilungamo chanu nʼchamuyaya, ndipo malamulo anu nʼchoona.

[143] Mavuto ndi masautso zandigwera, koma ndimakondwera ndi malamulo anu.

[144] Umboni wanu ndi wabwino nthawi zonse; patseni nzeru zomvetsa zinthu kuti ine ndikhale ndi moyo. Kofu

[145] Ndimayitana ndi mtima wanga wonse; ndiyankheni Inu Yehova, ndipo ndidzamvera zophunzitsa zanu.

[146] Ndikuyitana kwa Inu; pulumutseni ndipo ndidzasunga umboni wanu.

[147] Ndimadzuka tambala asanalire kuti ndipemphe thandizo; chiyembekezo changa chili mʼmawu anu.

[148] Maso anga amakhala chipenyere nthawi yonse ya usiku, kuti ndithe kulingalira malonjezo anu.

[149] Imvani mawu anga molingana ndi chikondi chanu chosasinthika; Yehova sungani moyo wanga, molingana ndi malamulo anu.

[150] Iwo amene amakonza njira zoyipa andiyandikira, koma ali kutali ndi malamulo anu.

[151] Koma Inu Yehova muli pafupi, malamulo anu onse ndi woona.

[152] Ndinaphunzira kalekale kuchokera mʼmaumboni anu kuti maumboni amene munakhazikitsawo ndi amuyaya. Reshi

[153] Yangʼanani masautso anga ndipo mundipulumutse, pakuti sindinayiwale malamulo anu.

[154] Mundiyimirire pa mlandu wanga ndi kundiwombola; sungani moyo wanga molingana ndi lonjezo lanu.

[155] Chipulumutso chili kutali ndi anthu oyipa, pakuti iwowo safunafuna zophunzitsa zanu.

[156] Chifundo chanu Yehova nʼchachikulu; sungani moyo wanga molingana ndi malamulo anu.

[157] Adani amene akundizunza ndi ambiri, koma ine sindinatembenuke kuchoka pa umboni wanu.

[158] Ndimawayangʼana monyansidwa anthu opanda chikhulupiriro, popeza samvera mawu anu.

[159] Onani momwe ndimakondera malangizo anu; sungani moyo wanga, Inu Yehova, molingana ndi chikondi chanu chosanthika.

[160] Mawu anu onse ndi owona; malamulo anu onse olungama ndi amuyaya. Sini ndi Shini

[161] Olamulira amandizunza popanda chifukwa, koma mtima wanga umanjenjemera ndi mawu anu.

[162] Ine ndimakondwa ndi lonjezo lanu, ngati munthu amene wapeza chuma chambiri.

[163] Ndimadana ndi chinyengo, kwambiri ndimanyansidwa nacho, koma ndimakonda malamulo anu.

[164] Ndimakutamandani kasanu ndi kawiri pa tsiku pakuti malamulo anu ndi olungama.

[165] Amene amakonda malamulo anu ali ndi mtendere waukulu, ndipo palibe chimene chingawapunthwitse

[166] Ndikudikira chipulumutso chanu, Inu Yehova, ndipo ndimatsatira malamulo anu.

[167] Ndimamvera umboni wanu pakuti ndimawukonda kwambiri.

[168] Ndimamvera malangizo anu ndi umboni wanu, pakuti njira zanga zonse ndi zodziwika pamaso panu. Tawu

[169] Kulira kwanga kufike pamaso panu Yehova; patseni nzeru zomvetsa zinthu molingana ndi mawu anu.

[170] Kupempha kwanga kufike pamaso panu; pulumutseni molingana ndi lonjezo lanu.

[171] Matamando asefukire pa milomo yanga, pakuti Inu mumandiphunzitsa malamulo anu.

[172] Lilime langa liyimbe mawu anu, popeza malamulo anu onse ndi olungama.

[173] Dzanja lanu likhale lokonzeka kundithandiza pakuti ndasankha malangizo anu.

[174] Ndikufunitsitsa chipulumutso chanu Yehova, ndipo ndimakondwera ndi malamulo anu.

[175] Loleni kuti ndikhale ndi moyo kuti ndikutamandeni, ndipo malamulo anu andichirikize.

[176] Ndasochera ngati nkhosa yotayika, funafunani mtumiki wanu, pakuti sindinayiwale malamulo anu.

Masalimo — Chapters