[1] Adzuke Mulungu, adani ake amwazikane; adani ake athawe pamaso pake.
[2] Monga momwe mphepo imachotsera utsi; Inu muwawulutsire kutali. Monga phula limasungunukira pa moto, oyipa awonongeke pamaso pa Mulungu.
[3] Koma olungama asangalale ndi kukondwera pamaso pa Mulungu; iwo akondwere ndi kusangalala.
[4] Imbirani Mulungu imbirani dzina lake matamando, mukwezeni Iye amene amakwera pa mitambo; dzina lake ndi Yehova ndipo sangalalani pamaso pake.
[5] Atate wa ana amasiye, mtetezi wa akazi amasiye, ndiye Mulungu amene amakhala mʼmalo oyera.
[6] Mulungu amakhazikitsa mtima pansi osungulumwa mʼmabanja, amatsogolera amʼndende ndi kuyimba; koma anthu osamvera amakhala ku malo owuma a dziko lapansi.
[7] Pamene munatuluka kutsogolera anthu anu, Inu Mulungu, pamene munayenda kudutsa chipululu,
[8] dziko lapansi linagwedezeka, miyamba inakhuthula pansi mvula, pamaso pa Mulungu, Mmodzi uja wa ku Sinai. Pamaso pa Mulungu, Mulungu wa Israeli.
[9] Munapereka mivumbi yochuluka, Inu Mulungu; munatsitsimutsa cholowa chanu cholefuka.
[10] Anthu anu anakhala mʼmenemo ndipo munapatsa anthu osauka zimene zinkawasowa chifukwa cha ubwino wanu Mulungu.
[11] Ambuye analengeza mawu, ndipo gulu linali lalikulu la iwo amene anapita kukawafalitsa;
[12] “Mafumu ndi ankhondo anathawa mwaliwiro; mʼmisasa anthu anagawana zolanda pa nkhondo.
[13] Ngakhale mukugona pakati pa makola a ziweto, mapiko a nkhunda akutidwa ndi siliva, nthenga zake ndi golide wonyezimira.”
[14] Pamene Wamphamvuzonse anabalalitsa mafumu mʼdziko, zinali ngati matalala akugwa pa Zalimoni.
[15] Mapiri a Basani ndi mapiri aulemerero; mapiri a Basani, ndi mapiri a msonga zambiri.
[16] Muyangʼaniranji mwansanje inu mapiri a msonga zambiri, pa phiri limene Mulungu analisankha kuti azilamulira, kumene Yehova mwini adzakhalako kwamuyaya?
[17] Magaleta a Mulungu ndi osawerengeka, ndi miyandamiyanda; Ambuye wabwera kuchokera ku Sinai, walowa mʼmalo ake opatulika.
[18] Pamene Inu munakwera mmwamba, munatsogolera a mʼndende ambiri; munalandira mphatso kuchokera kwa anthu, ngakhale kuchokera kwa owukira, kuti Inu Mulungu, mukhale kumeneko.
[19] Matamando akhale kwa Ambuye, kwa Mulungu Mpulumutsi wathu amene tsiku ndi tsiku amasenza zolemetsa zathu.
[20] Mulungu wathu ndi Mulungu amene amapulumutsa; Ambuye Wamphamvuzonse ndiye amene amatipulumutsa ku imfa.
[21] Ndithu Mulungu adzaphwanya mitu ya adani ake, zipewa za ubweya za iwo amene amapitiriza kuchita machimo awo.
[22] Ambuye akunena kuti, “Ndidzawabweretsa kuchokera ku Basani; ndidzawabweretsa kuchokera ku nyanja zozama.
[23] Kuti muviyike mapazi anu mʼmagazi a adani anu, pamene malilime a agalu anu akudyapo gawo lawo.”
[24] Mayendedwe aulemu a anthu anu aonekera poyera, Inu Mulungu; mayendedwe olemekeza Mulungu wanga ndi Mfumu yanga yokalowa mʼmalo opatulika.
[25] Patsogolo pali oyimba nyimbo pakamwa, pambuyo pawo oyimba nyimbo ndi zipangizo; pamodzi ndi iwo pali atsikana akuyimba matambolini.
[26] Tamandani Mulungu mu msonkhano waukulu; tamandani Yehova mu msonkhano wa Israeli.
[27] Pali fuko lalingʼono la Benjamini, kuwatsogolera, pali gulu lalikulu la ana a mafumu a Yuda, ndiponso pali ana a mafumu a Zebuloni ndi Nafutali.
[28] Kungani mphamvu zanu Mulungu; tionetseni nyonga zanu, Inu Mulungu, monga munachitira poyamba.
[29] Chifukwa cha Nyumba yanu ku Yerusalemu, mafumu adzabweretsa kwa Inu mphatso.
[30] Dzudzulani chirombo pakati pa mabango, gulu la ngʼombe zazimuna pakati pa ana angʼombe a mitundu ya anthu. Mochititsidwa manyazi, abweretse mitanda ya siliva. Balalitsani anthu a mitundu ina amene amasangalatsidwa ndi nkhondo.
[31] Nthumwi zidzachokera ku Igupto; Kusi adzadzipereka yekha kwa Mulungu.
[32] Imbirani Mulungu Inu mafumu a dziko lapansi imbirani Ambuye matamando. q4 Sela
[33] Kwa Iye amene amakwera pa mitambo yakalekale ya mmwamba amene amabangula ndi mawu amphamvu.
[34] Lengezani za mphamvu za Mulungu, amene ulemerero wake uli pa Israeli amene mphamvu zake zili mʼmitambo.
[35] Ndinu woopsa, Inu Mulungu mʼmalo anu opatulika; Mulungu wa Israeli amapereka mphamvu ndi nyonga kwa anthu ake. Matamando akhale kwa Mulungu!