Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 4:09

[1] Mwa Inu Yehova, ine ndimathawiramo; musalole nʼkomwe kuti ndichititsidwe manyazi; mundipulumutse chifukwa cha chilungamo chanu.

[2] Tcherani khutu lanu kwa ine, bwerani msanga kudzandilanditsa; mukhale thanthwe langa lothawirapo, linga lolimba kundipulumutsa ine.

[3] Popeza Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa, chifukwa cha dzina lanu tsogolereni ndi kundiwongolera.

[4] Ndimasuleni mu msampha umene anditchera pakuti ndinu pothawirapo panga.

[5] Mʼmanja mwanu ndipereka mzimu wanga; womboleni Yehova Mulungu wachoonadi.

[6] Koma ine ndimadana nawo amene amamamatira mafano achabechabe; ine ndimadalira Yehova.

[7] Ndidzakondwa ndi kusangalala mʼchikondi chanu popeza Inu munaona masautso anga ndipo mumadziwa kuwawa kwa moyo wanga.

[8] Inu simunandipereke kwa mdani koma mwayika mapazi anga pa malo otakasuka.

[9] Mundichitire chifundo Inu Yehova pakuti ndili pa mavuto; maso anga akulefuka ndi chisoni, mʼmoyo mwanga ndi mʼthupi mwanga momwe mukupweteka.

[10] Moyo wanga ukunyeka chifukwa cha kuwawidwa mtima ndi zaka zanga chifukwa cha kubuwula; mphamvu zanga zatha chifuwa cha masautso, ndipo mafupa anga akulefuka.

[11] Chifukwa cha adani anga onse, ndine wonyozeka kwambiri ndi anansi anga; ndine chochititsa manyazi kwa abwenzi anga. Iwo amene amandiona mu msewu amandithawa.

[12] Ine ndinayiwalika kwa iwo ngati kuti ndinamwalira; ndakhala ngati mʼphika wosweka.

[13] Pakuti ine ndamva zonena zoyipa za anthu ambiri; zoopsa zandizungulira mbali zonse; iwo akukonza chiwembu kuti alimbane nane, kuti atenge moyo wanga.

[14] Koma ndikudalira Inu Yehova; ndikunena kuti, “Ndinu Mulungu wanga.”

[15] Masiku anga ali mʼmanja mwanu; ndipulumutseni kwa adani anga ndi kwa iwo amene akundithamangitsa.

[16] Walitsani nkhope yanu pa mtumiki wanu; pulumutseni mwa chikondi chanu chosatha.

[17] Yehova musalole kuti ndichite manyazi, pakuti ndalirira kwa Inu; koma oyipa achititsidwe manyazi ndipo agone chete mʼmanda.

[18] Milomo yawo yabodzayo ikhale chete, pakuti chifukwa cha kunyada ayankhula modzikuza kutsutsana ndi wolungama.

[19] Ndi waukulu ubwino wanu umene mwawasungira amene amakuopani, umene mumapereka anthu akuona kwa iwo amene amathawira kwa Inu.

[20] Mu mthunzi wa pamalo popezeka panu muwabisa, kuwateteza ku ziwembu za anthu; mʼmalo anu okhalamo mumawateteza kwa anthu owatsutsa.

[21] Matamando akhale kwa Yehova, pakuti anaonetsa chikondi chake chodabwitsa kwa ine pamene ndinali mu mzinda wozingidwa.

[22] Ndili mʼnkhawa zanga ndinati, “Ine ndachotsedwa pamaso panu!” Komabe Inu munamva kupempha chifundo kwanga pamene ndinapempha thandizo kwa Inu.

[23] Kondani Yehova oyera mtima ake onse! Yehova amasunga wokhulupirika koma amalanga kwathunthu anthu odzikuza.

[24] Khalani ndi nyonga ndipo limbani mtima, inu nonse amene mumayembekezera Yehova.

Masalimo — Chapters