[1] Fuwulani kwa Mulungu ndi chimwemwe, dziko lonse lapansi!
[2] Imbani ulemerero wa dzina lake; kumutamanda kwake kukhale kwaulemerero.
[3] Nenani kwa Mulungu, “Ntchito zanu ndi zoopsa ndithu! Mphamvu yanu ndi yayikulu kwambiri kotero kuti adani anu amawerama pamaso panu.
[4] Dziko lonse lapansi limaweramira inu; limayimba matamando kwa Inu; limayimba matamando pa dzina lanu.” q4 Sela.
[5] Bwerani mudzaone zimene Mulungu wachita, ntchito zanu ndi zoopsa ndithu pakati pa anthu.
[6] Iye anasandutsa nyanja kukhala malo owuma, iwo anawoloka pa madzi ndi mapazi. Bwerani, tiyeni tikondwere mwa Iye.
[7] Iye amalamulira ndi mphamvu zake mpaka muyaya, maso ake amayangʼanira anthu a mitundu ina. Anthu owukira asadzitukumule.
[8] Tamandani Mulungu wathu, inu mitundu ya anthu, mulole kuti mawu a matamando ake amveke;
[9] Iye watchinjiriza miyoyo yathu ndi kusunga mapazi athu kuti angaterereke.
[10] Pakuti Inu Mulungu munatiyesa; munatiyenga ngati siliva.
[11] Inu mwatilowetsa mʼndende ndi kutisenzetsa zolemera pa misana yathu.
[12] Inu munalola kuti anthu akwere pa mitu yathu; ife tinadutsa mʼmoto ndi mʼmadzi, koma Inu munatibweretsa ku malo a zinthu zochuluka.
[13] Ine ndidzabwera ku Nyumba yanu ndi nsembe zopsereza ndi kukwaniritsa malumbiro anga.
[14] Malumbiro amene milomo yanga inalonjeza ndi pakamwa panga panayankhula pamene ndinali pa mavuto.
[15] Ndidzapereka nsembe nyama zonenepa kwa Inu ndi chopereka cha nkhosa zazimuna; ndidzapereka ngʼombe zamphongo ndi mbuzi. q4 Sela
[16] Bwerani ndipo mudzamve inu nonse amene mumaopa Mulungu. Ndidzakuwuzani zimene Iyeyo wandichitira.
[17] Ndinafuwula kwa Iye ndi pakamwa panga, matamando ake anali pa lilime panga.
[18] Ndikanasekerera tchimo mu mtima mwanga Ambuye sakanamvera;
[19] koma ndithu Mulungu wamvetsera ndipo watchera khutu ku mawu a kupempha kwanga.
[20] Matamando akhale kwa Mulungu amene sanakane pemphero langa kapena kuletsa chikondi chake pa ine!