Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 0:58

[1] Fulumirani Mulungu kundipulumutsa; Yehova bwerani msanga kudzandithandiza.

[2] Iwo amene akufunafuna moyo wanga achititsidwe manyazi ndi kusokonezedwa; onse amene akukhumba chiwonongeko changa abwezedwe mopanda ulemu.

[3] Onse amene akunena kwa ine kuti, “Aha, aha,” abwerere chifukwa cha manyazi awo.

[4] Koma onse amene akufunafuna Inu akondwere ndi kusangalala mwa Inu; iwo amene amakonda chipulumutso chanu nthawi zonse anene kuti, “Mulungu akuzike!”

[5] Koma ine ndine wosauka ndi wosowa; bwerani msanga kwa ine Inu Mulungu. Inu ndinu thandizo langa ndi momboli wanga; Inu Yehova musachedwe.

Masalimo — Chapters