Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:49

[1] Landitseni kwa adani anga, Inu Mulungu; munditeteze kwa anthu amene auka kutsutsana nane.

[2] Landitseni kwa anthu ochita zoyipa ndipo mundipulumutse kwa anthu okhetsa magazi.

[3] Onani momwe iwo akundibisalira! Anthu owopsa agwirizana zolimbana nane; osati chifukwa cha mlandu kapena tchimo langa, Inu Yehova.

[4] Ine sindinachite cholakwa, koma iwo ndi okonzeka kundithira nkhondo. Dzukani kuti mundithandize; penyani mavuto anga!

[5] Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, dzidzutseni nokha kuti mulange anthu a mitundu ina yonse; musaonetse chifundo chanu kwa anthu oyipa achinyengowa.

[6] Iwo amabweranso madzulo akuchita phokoso ngati agalu ndi kumangoyendayenda mu mzinda.

[7] Onani zomwe amalavula mʼkamwa mwawo; iwo amalavula malupanga kuchokera pa milomo yawo, ndipo amanena kuti, “Ndani angatimve?”

[8] Koma Inu Yehova, mumawaseka, mumayinyoza mitundu yonseyo.

[9] Inu mphamvu yanga, ine ndiyangʼana kwa inu; Inu Mulungu, ndinu linga langa.

[10] Mulungu wanga wachikondi. Mulungu adzapita patsogolo panga ndipo adzandilola kunyada pa iwo amene amandinyoza.

[11] Koma musawaphe, Inu Ambuye chishango chathu, kuopa kuti anthu anga angayiwale. Mwa mphamvu zanu, lolani kuti azingoyendayenda ndipo muwatsitse.

[12] Chifukwa cha machimo a pakamwa pawo chifukwa cha mawu a milomo yawo, iwo akodwe mʼkunyada kwawo. Chifukwa cha matemberero ndi mabodza amene ayankhula

[13] muwawononge mu ukali (wanu) muwawononge mpaka atheretu. Pamenepo zidzadziwika ku malekezero a dziko lapansi kuti Mulungu amalamulira Yakobo.

[14] Iwo amabweranso madzulo, akuchita phokoso ngati agalu ndi kumangoyenda mu mzinda.

[15] Iwo amayendayenda kufuna chakudya ndipo amawuwa ngati sanakhute.

[16] Koma ine ndidzayimba za mphamvu yanu, mmawa ndidzayimba zachikondi chanu; pakuti ndinu linga langa, pothawirapo panga mʼnthawi ya mavuto.

[17] Inu mphamvu yanga, ndiyimba matamando kwa inu; Inu Mulungu, ndinu linga langa, Mulungu wanga wachikondi.

Masalimo — Chapters