Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:01

[1] Pamene Israeli anatuluka mu Igupto, nyumba ya Yakobo kuchoka ku mtundu wa anthu a chiyankhulo chachilendo,

[2] Yuda anasanduka malo opatulika a Mulungu, Israeli anasanduka ufumu wake.

[3] Nyanja inaona ndi kuthawa, mtsinje wa Yorodani unabwerera mʼmbuyo;

[4] mapiri analumphalumpha ngati nkhosa zazimuna, timapiri ngati ana ankhosa.

[5] Nʼchifukwa chiyani iwe unathawa? iwe mtsinje wa Yorodani unabwereranji mʼmbuyo?

[6] inu mapiri, munalumphalumphiranji ngati nkhosa zazimuna, inu timapiri, ngati ana ankhosa?

[7] Njenjemera pamaso pa Ambuye iwe dziko lapansi, pamaso pa Mulungu wa Yakobo,

[8] amene anasandutsa thanthwe kukhala chitsime, thanthwe lolimba kukhala akasupe a madzi.

Masalimo — Chapters