Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:01

[1] Uthenga uli mu mtima mwanga wonena za kuchimwa kwa munthu woyipa: Mu mtima mwake mulibe kuopa Mulungu.

[2] Pakuti iye mʼkuona kwake amadzinyenga yekha kwambiri, sazindikira kapena kudana ndi tchimo lake.

[3] Mawu a pakamwa pake ndi oyipa ndi achinyengo; iyeyo waleka kukhala wanzeru ndi kuchita zabwino.

[4] Ngakhale ali pa bedi pake amakonzekera zoyipa; iye amadzipereka yekha ku njira ya uchimo ndipo sakana cholakwa chilichonse.

[5] Chikondi chanu Yehova, chimafika ku mayiko a kumwamba, kukhulupirika kwanu mpaka ku mitambo.

[6] Chilungamo chanu Mulungu chili ngati mapiri aakulu, chiweruzo chanu chili ngati kuzama kwakukulu. Yehova mumasunga munthu pamodzi ndi chinyama.

[7] Chikondi chanu chosatha ndi chamtengowapatali! Otchuka pamodzi ndi anthu wamba pakati pa anthu amapeza pothawirapo mu mthunzi wa mapiko anu.

[8] Iwo amadyerera zinthu zambiri za mʼnyumba yanu; Inu mumawapatsa chakumwa kuchokera mu mtsinje wanu wachikondwerero.

[9] Pakuti kwa Inu kuli kasupe wamoyo; mʼkuwala kwanu ifenso timaona kuwala.

[10] Pitirizani chikondi chanu pa iwo amene amakudziwani, chilungamo chanu kwa olungama mtima.

[11] Musalole kuti phazi la wodzikuza libwere kulimbana nane, kapena dzanja la oyipa kundithamangitsa.

[12] Onani momwe ochita zoyipa agonera atagwa, aponyeni pansi, kuti asathe kudzukanso!

Masalimo — Chapters