[1] Nʼchifukwa chiyani mwatitaya ife kwamuyaya, Inu Mulungu? Chifukwa chiyani mkwiyo wanu ukutukutira pa nkhosa za busa lanu?
[2] Kumbukirani anthu amene munawagula kalekale, fuko la cholowa chanu, limene Inu munaliwombola, phiri la Ziyoni, kumene inuyo mumakhala.
[3] Tembenuzani mapazi kuloza ku mabwinja awa amuyaya chiwonongeko ichi chonse mdani wabweretsa pa malo opatulika.
[4] Adani anu anabangula pa malo pamene Inu munkakumana nafe; anayimika mbendera zawo monga zizindikiro zachigonjetso.
[5] Iwo anachita ngati anthu oti anyamula mbendera zawo kuti adule mitengo mʼnkhalango.
[6] Kenaka anaphwanya ndi nkhwangwa ndi akasemasema awo zonse zimene tinapachika.
[7] Iwo anatentha malo anu opatulika mpaka kuwagwetsa pansi; anadetsa malo okhalamo dzina lanu.
[8] Ndipo anati mʼmitima yawo, “Tawatha kwathunthu.” Anatentha malo aliwonse amene Mulungu amapembedzedwerako mʼdzikomo.
[9] Ife sitinapatsidwe chizindikiro chodabwitsa; palibe aneneri amene atsala ndipo palibe aliyense wa ife akudziwa kuti izi zidzatenga nthawi yayitali bwanji.
[10] Kodi mpaka liti, mdani adzanyoze Inu Mulungu? Kodi amaliwongowa adzapeputsa dzina lanu kwamuyaya?
[11] Chifukwa chiyani mukubweza dzanja lanu lamanja? Litulutseni kuchoka pachifuwa chanu ndipo muwawononge!
[12] Koma Inu Mulungu, ndinu Mfumu yanga kuyambira kalekale; Mumabweretsa chipulumutso pa dziko lapansi.
[13] Ndinu amene munagawa nyanja ndi mphamvu yanu; munathyola mitu ya zirombo za mʼmadzi.
[14] Ndinu amene munaphwanya mitu ya Leviyatani ndi kuyipereka ngati chakudya cha zirombo za mʼchipululu.
[15] Ndinu amene munatsekula akasupe ndi mitsinje, munawumitsa mitsinje imene siphwa nthawi zonse.
[16] Masana ndi anu ndipo usiku ndi wanunso; Inuyo munakhazikitsa dzuwa ndi mwezi.
[17] Ndinu amene munakhazikitsa malire onse a dziko lapansi; munakhazikitsa chilimwe ndi dzinja.
[18] Kumbukirani momwe mdani wakunyozerani Inu Yehova, momwe anthu opusa apeputsira dzina lanu.
[19] Musapereke moyo wa nkhunda yanu ku zirombo zakuthengo; nthawi zonse musayiwale miyoyo ya anthu anu osautsidwa.
[20] Mukumbukire pangano lanu, pakuti malo obisika a mʼdziko asanduka mochitira zachiwawa zochuluka.
[21] Musalole kuti osautsidwa abwerere mwamanyazi; osauka ndi osowa atamande dzina lanu.
[22] Dzukani Inu Mulungu ndipo dzitetezeni pa mlandu; kumbukirani momwe opusa akukunyozerani tsiku lonse.
[23] Musalekerere phokoso la otsutsana nanu, chiwawa cha adani anu, chimene chikumveka kosalekeza.