[1] Matamando akudikira Inu Mulungu mu Ziyoni; kwa inu malumbiro athu adzakwaniritsidwa.
[2] Inu amene mumamva pemphero, kwa inu anthu onse adzafika.
[3] Pamene tinathedwa nzeru ndi machimo, Inu munakhululukira mphulupulu zathu.
[4] Odala iwo amene inu muwasankha ndi kuwabweretsa pafupi kukhala mʼmabwalo anu! Ife tadzazidwa ndi zinthu zabwino za mʼNyumba mwanu, za mʼNyumba yanu yoyera.
[5] Mumatiyankha ife ndi ntchito zodabwitsa zachilungamo, Inu Mulungu Mpulumutsi wathu, chiyembekezo cha mathero onse a dziko lapansi ndi cha nyanja zomwe zili kutali kwambiri,
[6] amene munapanga mapiri ndi mphamvu zanu, mutadziveka nokha ndi mphamvu.
[7] Amene munakhalitsa bata nyanja kukokoma kwa mafunde ake, ndi phokoso la anthu a mitundu ina.
[8] Iwo amene akukhala kutali amaopa zizindikiro zozizwitsa zanu; kumene dzuwa limatulukira ndi kumene dzuwa limalowera. Inu mumafuna nyimbo zachimwemwe.
[9] Inu mumasamalira dziko lapansi ndi kulithirira; Inuyo mumalilemeretsa kwambiri. Mtsinje wa Mulungu ndi wodzaza ndi madzi kuti upereke tirigu kwa anthu, pakuti Inu munakhazikitsa zimenezi.
[10] Mwadzaza nthaka yake ndi madzi ndi kusalaza migula yake, mwayifewetsa ndi mvula yamawawa ndi kudalitsa mbewu zake.
[11] Inu mumaveka chaka ndi zinthu zochuluka, ndipo ngolo zanu zimasefukira ndi zinthu zochuluka.
[12] Malo a udzu a mʼchipululu amasefukira; mapiri avekedwa ndi chisangalalo.
[13] Madambo akutidwa ndi zoweta ndi zigwa zavekedwa ndi tirigu; izo pamodzi zikufuwula ndi kuyimba mwachimwemwe.