[1] Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino. Pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
[2] Yamikani Mulungu wa milungu. Pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
[3] Yamikani Ambuye wa ambuye, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
[4] Iye yekhayo amene amachita zodabwitsa zazikulu, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
[5] Amene mwachidziwitso chake anapanga mayiko akumwamba, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
[6] Amene anayala dziko lapansi pamwamba pa madzi, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
[7] Amene anapanga miyuni ikuluikulu, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
[8] Dzuwa lilamulire usana, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
[9] Mwezi ndi nyenyezi zilamulire usiku, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
[10] Amene anakantha ana woyamba kubadwa a Igupto, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
[11] Natulutsa Israeli pakati pawo, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
[12] Ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasuka, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
[13] Amene anagawa Nyanja Yofiira pakati, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
[14] Nadutsitsa Israeli pakati pa nyanjayo, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
[15] Koma anakokolola Farao ndi ankhondo ake mʼNyanja Yofiira, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
[16] Amene anatsogolera anthu ake mʼchipululu pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
[17] Amene anakantha mafumu akuluakulu, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
[18] Napha mafumu amphamvu, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
[19] Siloni mfumu ya Aamori, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
[20] Ogi mfumu ya Basani, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
[21] Napereka dziko lawo ngati cholowa, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
[22] Cholowa cha mtumiki wake Israeli; pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
[23] Amene anatikumbukira ife anthu opeputsidwa, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
[24] Amene anatimasula kwa adani athu, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
[25] Amene amapereka chakudya kwa cholengedwa chilichonse, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
[26] Yamikani Mulungu wakumwamba, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.