[1] Mulungu ndi wabwino ndithu kwa Israeli, kwa iwo amene ndi oyera mtima.
[2] Koma kunena za ine, mapazi anga anali pafupi kuterereka; ndinatsala pangʼono kugwa.
[3] Pakuti ndinkachitira nsanje odzitamandira, pamene ndinaona mtendere wa anthu oyipa.
[4] Iwo alibe zosautsa; matupi awo ndi athanzi ndi amphamvu.
[5] Saona mavuto monga anthu ena; sazunzika ngati anthu ena onse.
[6] Nʼchifukwa chake kunyada kuli monga mkanda wa mʼkhosi mwawo; amadziveka chiwawa.
[7] Mʼmitima yawo yokhota mumachokera zolakwa; zoyipa zochokera mʼmaganizo awo sizidziwa malire.
[8] Iwowo amanyogodola ndi kumayankhula zoyipa; mwa kudzikuza kwawo amaopseza ena nʼkumati, “Tikuponderezani.”
[9] Pakamwa pawo pamayankhula monyoza Mulungu kumwamba ndipo lilime lawo limayenda pa dziko lapansi.
[10] Nʼchifukwa chake anthu awo amapita kwa iwowo ndi kumwa madzi mochuluka.
[11] Iwo amati, “Kodi Mulungu angadziwe bwanji? Kodi Wammwambamwamba angadziwe kalikonse?”
[12] Umu ndi mmene oyipa alili; nthawi zonse ali pabwino ndipo chuma chawo chimachulukirachulukira.
[13] Ndithudi ine ndawusunga pachabe mtima wanga woyera; pachabe ndasamba mʼmanja mwanga mwa kusalakwa kwanga.
[14] Tsiku lonse ndapeza mavuto; ndakhala ndi kulangidwa mmawa uliwonse.
[15] Ndikanati, “Ndidzayankhula motere,” ndikanachita chosakhulupirika kwa ana anu.
[16] Pamene ndinayesa kuti ndimvetse zonsezi, zinandisautsa kwambiri
[17] kufikira nditalowa mʼmalo opatulika a Mulungu; pamenepo ndinamvetsa mathero awo.
[18] Zoonadi Inu munawayika pa malo woterera; Mumawagwetsa pansi kuti awonongeke.
[19] Mwamsangamsanga iwo amawonongedwa, amasesedwa kwathunthu ndi mantha!
[20] Monga loto pamene wina adzuka, kotero pamene Inu muuka, Inu Ambuye, mudzawanyoza ngati maloto chabe.
[21] Pamene mtima wanga unasautsidwa ndi kuwawidwa mu mzimu mwanga,
[22] ndinali wopusa ndi wosadziwa; ndinali chirombo chopanda nzeru pamaso panu.
[23] Komabe ineyo ndili ndi Inu nthawi zonse; mumandigwira dzanja langa lamanja.
[24] Inu mumanditsogolera ndi malangizo anu ndipo pambuyo pake mudzanditenga ku ulemerero.
[25] Kodi kumwamba ndili ndi yani kupatula Inu? Ndipo dziko lapansi lilibe chilichonse chimene ndimachilakalaka koposa Inuyo.
[26] Thupi ndi mtima wanga zitha kufowoka, koma Mulungu ndiye mphamvu ya mtima wanga ndi cholandira changa kwamuyaya.
[27] Iwo amene ali kutali ndi Inu adzawonongeka; Inu mumawononga onse osakhulupirika pamaso panu.
[28] Koma kunena za Ine ndi kwabwino kukhala pafupi ndi Mulungu. Ndatsimikiza kuti Ambuye Yehova ndiwo pothawirapo panga ndipo ndidzalalika ntchito zanu zonse.