Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 0:58

[1] Mpaka liti Yehova? Kodi mudzandiyiwala mpaka kalekale? Mpaka liti mudzandibisira nkhope yanu?

[2] Ndidzalimbana ndi maganizo anga ndi kukhala ndi chisoni mu mtima mwanga tsiku lililonse mpaka liti? Mpaka liti adani anga adzandipambana?

[3] Ndiyangʼaneni ndi kundiyankha, Inu Yehova Mulungu wanga. Walitsani maso anga kuti ndingafe;

[4] mdani wanga adzati, “Ndamugonjetsa,” ndipo adani anga adzakondwera pamene ine ndagwa.

[5] Koma ndikudalira chikondi chanu chosasinthika; mtima wanga umakondwera ndi chipulumutso chanu.

[6] Ine ndidzayimbira Yehova pakuti wandichitira zokoma.

Masalimo — Chapters