Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:13

[1] Ndikulirira Yehova mofuwula; ndikukweza mawu anga kwa Yehova kupempha chifundo.

[2] Ndikukhuthula madandawulo anga pamaso pake; ndikufotokoza za masautso anga pamaso pake.

[3] Pamene mzimu wanga walefuka mʼkati mwanga, ndinu amene mudziwa njira yanga. Mʼnjira imene ndimayendamo anthu anditchera msampha mobisa.

[4] Yangʼanani kumanja kwanga ndipo onani; palibe amene akukhudzika nane. Ndilibe pothawira; palibe amene amasamala za moyo wanga.

[5] Ndilirira Inu Yehova; ndikuti, “Ndinu pothawirapo panga, gawo langa mʼdziko la anthu amoyo.”

[6] Mverani kulira kwanga pakuti ndathedwa nzeru; pulumutseni kwa amene akundithamangitsa pakuti ndi amphamvu kuposa ine.

[7] Tulutseni mʼndende yanga kuti nditamande dzina lanu. Ndipo anthu olungama adzandizungulira chifukwa cha zabwino zanu pa ine.

Masalimo — Chapters