Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 6:06

[1] Yamikani Yehova, itanani dzina lake; lalikirani pakati pa anthu a mitundu ina zimene Iye wachita.

[2] Imbirani Iye, imbani matamando kwa Iyeyo; fotokozani za machitidwe ake onse odabwitsa.

[3] Munyadire dzina lake loyera; mitima ya iwo amene amafunafuna Yehova ikondwere.

[4] Dalirani Yehova ndi mphamvu zake; funafunani nkhope yake nthawi yonse.

[5] Kumbukirani zodabwitsa zimene Iye anazichita, zozizwitsa zake ndi maweruzo amene anapereka,

[6] inu zidzukulu za Abrahamu mtumiki wake, inu ana a Yakobo, osankhika ake.

[7] Iye ndiye Yehova Mulungu wathu; maweruzo ake ali pa dziko lonse lapansi.

[8] Iyeyo amakumbukira pangano lake kwamuyaya, mawu amene analamula kwa mibado yonse,

[9] pangano limene Iye anapanga ndi Abrahamu, lumbiro limene analumbira kwa Isake.

[10] Iye analitsimikiza kwa Yakobo monga zophunzitsa, kwa Israeli monga pangano lamuyaya:

[11] “Ndidzapereka kwa iwe dziko la Kanaani ngati gawo la cholowa chako.”

[12] Pamene iwo anali ngati anthu ochepa mʼchiwerengero, ochepa ndithu, ndiponso alendo mʼdzikolo,

[13] ankayendayenda kuchoka ku mtundu wina wa anthu ndi kupita ku mtundu wina, kuchoka mu ufumu wina kupita ku wina.

[14] Iye sanalole wina aliyense kuwapondereza; anadzudzula mafumu chifukwa cha iwo:

[15] “Musakhudze odzozedwa anga; musachitire choyipa aneneri anga.”

[16] Iye anabweretsa njala pa dziko ndipo anawononga chakudya chonse;

[17] Iyeyo anatumiza munthu patsogolo pawo, Yosefe anagulitsidwa ngati kapolo.

[18] Iwo anavulaza mapazi ake ndi matangadza, khosi lake analiyika mʼzitsulo,

[19] mpaka zimene Iye ananeneratu zitakwaniritsidwa, mpaka mawu a Yehova ataonetsa kuti Iye ananena zoona.

[20] Mfumu inatuma munthu kukamumasula, wolamulira wa mitundu ya anthu anamasula iyeyo.

[21] Anamuyika kukhala wolamulira nyumba yake, wolamulira zonse zimene iye anali nazo,

[22] kulangiza ana a mfumu monga ankafunira ndi kuphunzitsa nzeru akuluakulu.

[23] Tsono Israeli analowa mu Igupto; Yakobo anakhala monga mlendo mʼdziko la Hamu.

[24] Yehova anachulukitsa anthu ake; ndipo anachititsa kuti akhale ochuluka kwambiri kuposa adani awo;

[25] amene mitima yawo anayitembenuza kuti idane ndi anthu ake, kukonzera chiwembu atumiki ake.

[26] Yehova anatuma Mose mtumiki wake, ndi Aaroni amene Iye anamusankha.

[27] Iwo anachita zizindikiro zozizwitsa pakati pawo, zodabwitsa zake mʼdziko la Hamu.

[28] Yehova anatumiza mdima nasandutsa dziko kuti likhale la mdima. Koma anthuwo anakaniratu mawu a Yehova.

[29] Yehova anasandutsa madzi awo kukhala magazi, kuchititsa kuti nsomba zawo zife.

[30] Dziko lawo linadzaza ndi achule amene analowa mʼzipinda zogona za olamulira awo.

[31] Iye anayankhula, ndipo kunabwera ntchentche zochuluka ndi nsabwe mʼdziko lawo lonse.

[32] Iyeyo anatembenuza mvula yawo kukhala matalala, ndi zingʼaningʼani mʼdziko lawo lonse;

[33] Anagwetsa mitengo yawo ya mpesa ndi mitengo yawo ya mkuyu, nawononganso mitengo ina ya mʼdziko lawolo.

[34] Iye anayankhula, ndipo dzombe linabwera, ziwala zosawerengeka;

[35] zinadya chilichonse chobiriwira cha mʼdziko lawo, zinadya zonse zotuluka mʼnthaka yawo.

[36] Kenaka anakantha ana onse oyamba kubadwa a mʼdziko lawo, zipatso zoyamba za umunthu wawo wonse.

[37] Yehova anatulutsa Israeli, atatenga siliva ndi golide wambiri, ndipo pakati pa mafuko awo palibe mmodzi amene anafowoka.

[38] Dziko la Igupto linakondwa pamene iwo anachoka, pakuti kuopsa kwa Israeli kunawagwera iwo.

[39] Iye anatambasula mitambo ngati chofunda chawo, ndi moto owawunikira usiku.

[40] Iwo anapempha, ndipo Iye anawabweretsera zinziri ndipo anawakhutitsa ndi chakudya chochokera kumwamba.

[41] Iye anatsekula thanthwe, ndipo madzi anatuluka; ngati mtsinje anayenda mʼchipululu.

[42] Pakuti anakumbukira lonjezo lake loyera limene linaperekedwa kwa Abrahamu mtumiki wake.

[43] Iye anatulutsa anthu ake akukondwera, osankhika ake akufuwula mwachimwemwe;

[44] Iye anawapatsa mayiko a anthu a mitundu ina ndipo anakhala olowamʼmalo a zimene ena anazivutikira,

[45] kuti iwo asunge malangizo ake ndi kutsatira malamulo ake. Tamandani Yehova.

Masalimo — Chapters