Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:43

[1] Ndisungeni Inu Mulungu, pakuti ine ndimathawira kwa Inu.

[2] Ndinati kwa Yehova, “Inu ndinu Ambuye anga; popanda Inu, ine ndilibe chinthu chinanso chabwino.”

[3] Kunena za oyera mtima amene ali pa dziko, amenewa ndi olemekezeka, amene ndimakondwera nawo.

[4] Anthu amene amathamangira kwa milungu ina mavuto awo adzachulukadi. Ine sindidzathira nawo nsembe zawo zamagazi kapena kutchula mayina awo ndi pakamwa panga.

[5] Yehova, Inu mwandipatsa cholowa changa ndi chikho changa; mwateteza kolimba gawo langa.

[6] Malire a malo anga akhala pabwino; ndithudi, ine ndili cholowa chokondweretsa kwambiri.

[7] Ine ndidzatamanda Yehova amene amandipatsa uphungu; ngakhale usiku mtima wanga umandilangiza.

[8] Ndayika Yehova patsogolo panga nthawi zonse. Popeza Iyeyo ali kudzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.

[9] Choncho mtima wanga ndi wosangalala ndipo pakamwa panga pakukondwera; thupi langanso lidzakhala pabwino,

[10] chifukwa Inu simudzandisiya ku manda, simudzalola kuti woyera wanu avunde.

[11] Inu mwandidziwitsa njira ya moyo; mudzandidzaza ndi chimwemwe pamaso panu, ndidzasangalala mpaka muyaya pa dzanja lanu lamanja.

Masalimo — Chapters