[1] Ombani mʼmanja, inu anthu onse; fuwulani kwa Mulungu ndi mawu achimwemwe.
[2] Ndi woopsadi Yehova Wammwambamwamba; Mfumu yayikulu ya dziko lonse lapansi!
[3] Iye anatigonjetsera mitundu yambirimbiri ya anthu; anayika anthu pansi pa mapazi athu.
[4] Iye anatisankhira cholowa chathu, chonyaditsa cha Yakobo, amene anamukonda. q4 Sela
[5] Mulungu wakwera, anthu akumufuwulira mwachimwemwe, Yehova wakwera, akumuyimbira malipenga.
[6] Imbani matamando kwa Mulungu, imbani matamando; imbani matamando kwa mfumu yathu, imbani matamando.
[7] Pakuti Mulungu ndi mfumu ya dziko lonse lapansi; imbirani Iye salimo la matamando.
[8] Mulungu akulamulira mitundu ya anthu; Mulungu wakhala pa mpando wake waufumu woyera.
[9] Anthu otchuka mwa anthu a mitundu ina asonkhana monga anthu a Mulungu wa Abrahamu, pakuti mafumu a dziko lapansi ndi ake a Mulungu; Iye wakwezedwa kwakukulu.