[1] Bwerani, tiyeni timuyimbire Yehova mwachimwemwe, tiyeni tifuwule kwa Thanthwe la chipulumutso chathu
[2] Tiyeni tibwere pamaso pake ndi chiyamiko ndipo mupembedzeni Iyeyo ndi zida zoyimbira ndi nyimbo.
[3] Pakuti Yehova ndi Mulungu wamkulu, mfumu yayikulu pamwamba pa milungu yonse.
[4] Mʼmanja mwake muli maziko ozama a dziko lapansi, ndipo msonga za mapiri ndi zake.
[5] Nyanja ndi yake, pakuti anayilenga ndi Iye, ndipo manja ake anawumba mtunda wowuma.
[6] Bwerani, tiyeni tiwerame pomulambira, tiyeni tigwade pamaso pa Yehova Mlengi wathu;
[7] pakuti Iye ndiye Mulungu wathu ndipo ife ndife anthu a pabusa pake, ndi nkhosa za mʼdzanja lake. Lero ngati inu mumva mawu ake,
[8] musawumitse mitima yanu monga momwe munachitira pa Meriba, monga munachitira tsiku lija pa Masa mʼchipululu.
[9] Kumene makolo anu anandiyesa ndi kundiputa, ngakhale anaona zimene Ine ndinazichita.
[10] Kwa zaka makumi anayi ndinali wokwiya ndi mʼbado umenewo; ndipo ndinati, “Iwo ndi anthu amene mitima yawo imasochera ndipo sanadziwe njira zanga.”
[11] Choncho ndili chikwiyire, ndinalumbira kuti, “Iwowa sadzalowa ku malo anga a mpumulo.”