Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 5:50

[1] Usamavutike chifukwa cha anthu oyipa kapena kuchitira nsanje amene akuchita cholakwa;

[2] pakuti monga udzu iwo adzafota msanga, ngati mbewu zobiriwira adzanyala msanga.

[3] Khulupirira Yehova ndipo uzichita zabwino; khazikika mʼdziko ndi kutsata zokhulupirika.

[4] Udzikondweretse wekha mwa Yehova ndipo Iye adzakupatsa zokhumba za mtima wako.

[5] Pereka njira yako kwa Yehova; dalira Iye ndipo Iyeyo adzachita izi:

[6] Iye adzachititsa chilungamo chako kuwala ngati mʼbandakucha, chiweruzo chako ngati dzuwa la masana.

[7] Khala chete pamaso pa Yehova ndipo umudikire mofatsa; usavutike pamene anthu apambana mʼnjira zawo, pamene iwo achita zinthu zawo zoyipa.

[8] Pewa kupsa mtima ndipo tembenuka kuchoka ku ukali, usavutike chifukwa zimenezi zimatsogolera ku zoyipa.

[9] Pakuti anthu oyipa adzachotsedwa, koma iwo amene amayembekeza mwa Yehova adzalandira dziko.

[10] Kwa kanthawi oyipa sadzapezekanso; ngakhale muwafunefune, sadzapezekanso.

[11] Koma ofatsa adzalandira dziko ndipo adzasangalala ndi mtendere waukulu.

[12] Oyipa amakonza chiwembu kutsutsana ndi olungama ndipo amawakukutira mano;

[13] koma Ambuye amaseka oyipa pakuti Iye amadziwa kuti tsiku lawo likubwera.

[14] Oyipa amasolola lupanga ndi kupinda uta kugwetsa osauka ndi osowa, kupha iwo amene njira zawo ndi zolungama.

[15] Koma malupanga awo analasa mitima yawo yomwe, ndipo mauta awo anathyoka.

[16] Zabwino zochepa zimene olungama ali nazo ziposa chuma cha anthu oyipa ambiri;

[17] pakuti mphamvu ya oyipa idzasweka, koma Yehova amasunga olungama.

[18] Masiku a anthu osalakwa amadziwika ndi Yehova, ndipo cholowa chawo chidzakhala mpaka muyaya.

[19] Pa nthawi ya mavuto iwo sadzafota; mʼmasiku a njala adzakhala ndi zinthu zambiri.

[20] Koma oyipa adzawonongeka; adani a Yehova adzakhala ngati kukongola kwa kuthengo, iwo adzazimirira ngati utsi.

[21] Oyipa amabwereka ndipo sabweza koma olungama amapereka mowolowamanja.

[22] Iwo amene Yehova amawadalitsa adzalandira dziko, koma amene Iye amawatemberera adzachotsedwa.

[23] Ngati Yehova akondwera ndi njira ya munthu, amakhazikitsa mayendedwe ake;

[24] ngakhale atapunthwa sadzagwa, pakuti Yehova amamutchinjiriza ndi dzanja lake.

[25] Ine ndinali wamngʼono ndipo tsopano ndakalamba koma sindinaonepo olungama akusiyidwa kapena ana awo akupempha chakudya.

[26] Iwo ndi owolowamanja nthawi zonse ndipo amabwereketsa mwaufulu; ana awo adzadalitsika.

[27] Tembenuka kuchoka ku zoyipa ndipo chita zabwino; pamenepo udzakhazikika mʼdziko kwamuyaya.

[28] Pakuti Yehova amakonda wolungama ndipo sadzasiya okhulupirika ake. Iwo adzatetezedwa kwamuyaya, koma zidzukulu za oyipa zidzachotsedwa;

[29] olungama adzalandira dziko ndipo adzakhazikikamo kwamuyaya.

[30] Pakamwa pa munthu wolungama pamayankhula za nzeru, ndipo lilime lake limayankhula zolungama.

[31] Lamulo la Mulungu wake lili mu mtima mwake; mapazi ake saterereka.

[32] Oyipa amabisala kudikira olungama; kufunafuna miyoyo yawoyo;

[33] koma Yehova sadzawasiya pansi pa mphamvu yawo kapena kuti atsutsidwe pamene abweretsedwa pa milandu.

[34] Khulupirira Yehova, ndipo sunga njira yake; Iye adzakukweza ndipo udzalandira dziko kuti likhale lako; udzaona anthu oyipa akuwonongeka.

[35] Ine ndinaona munthu woyipa ndi munthu wopanda chifundo akupeza bwino ngati mtengo wobiriwira pa nthaka ya makolo ake.

[36] Koma sanachedwe kumwalira ndipo sanaonekenso; ngakhale ndinamuyangʼanayangʼana, sanapezekenso.

[37] Ganizira za munthu wosalakwa, yangʼanitsitsa munthu wolungama; udzaona kuti ali ndi tsogolo labwino ndipo ali ndi zidzukulu zambiri.

[38] Koma anthu ochimwa adzawonongeka; iwowo pamodzi ndi zidzukulu zawo zomwe.

[39] Chipulumutso cha olungama chimachokera kwa Yehova; Iye ndiye linga lawo pa nthawi ya masautso.

[40] Yehova amawathandiza ndi kuwalanditsa; Iye amawalanditsa kwa oyipa ndi kuwapulumutsa, pakuti amathawira kwa Iye.

Masalimo — Chapters