Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:00

[1] Ngodala munthu amene zolakwa zake zakhululukidwa; amene machimo ake aphimbidwa.

[2] Ngodala munthu amene machimo ake Yehova sawawerengeranso pa iye ndipo mu mzimu mwake mulibe chinyengo.

[3] Pamene ndinali chete, mafupa anga anakalamba chifukwa cha kubuwula kwanga tsiku lonse.

[4] Pakuti usana ndi usiku dzanja lanu linandipsinja; mphamvu zanga zinatha monga nthawi yotentha yachilimwe. q4 Sela

[5] Kotero ine ndinavomereza tchimo langa kwa Inu, sindinabise mphulupulu zanga. Ndinati, “Ine ndidzawulula zolakwa zanga kwa Yehova, ndipo Inu munandikhululukira mlandu wa machimo anga.” q4 Sela

[6] Choncho aliyense okhulupirika apemphere kwa Inuyo pomwe mukupezeka; ndithu pamene madzi amphamvu auka, sadzamupeza.

[7] Inu ndi malo anga obisala; muzinditeteza ku mavuto ndipo muzindizinga ndi nyimbo zachipulumutso. q4 Sela

[8] Ndidzakulangiza ndi kukuphunzitsa njira imene udzayendamo; ndidzakupatsa uphungu ndi kukuyangʼanira.

[9] Usakhale ngati kavalo kapena bulu, zimene zilibe nzeru, koma ziyenera kuwongoleredwa ndi zitsulo za mʼkamwa ndi pamutu, ukapanda kutero sizibwera kwa iwe.

[10] Zowawa ndi zambiri za anthu oyipa koma chikondi chosatha cha Yehova chimamuzinga munthu amene amadalira Iye.

[11] Kondwerani mwa Yehova inu olungama; imbani, inu nonse amene muli owongoka mtima!

Masalimo — Chapters