Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:15

[1] Kwa Inu Yehova, ndipereka moyo wanga.

[2] Ndimadalira Inu Mulungu wanga. Musalole kuti ndichite manyazi kapena kuti adani anga andipambane.

[3] Aliyense amene amayembekezera kwa Ambuye sadzachititsidwa manyazi koma achinyengo ndiwo adzachititsidwe manyazi ndipo sadzakhala ndi chodzitetezera.

[4] Ndidziwitseni njira zanu Inu Yehova, phunzitseni mayendedwe anu;

[5] tsogolereni mʼchoonadi chanu ndi kundiphunzitsa, pakuti Inu ndinu Mulungu mpulumutsi wanga, ndipo chiyembekezo changa chili mwa Inu tsiku lonse.

[6] Kumbukirani Inu Yehova chifundo ndi chikondi chanu chachikulu, pakuti ndi zakalekale.

[7] Musakumbukire machimo a ubwana wanga ndi makhalidwe anga owukira; molingana ndi chikondi chanu ndikumbukireni ine, pakuti Inu Yehova ndinu wabwino.

[8] Yehova ndi wabwino ndi wolungama; choncho Iye akulangiza ochimwa mʼnjira yake.

[9] Amatsogolera odzichepetsa kuti achite zolungama ndipo amawaphunzitsa njira zake.

[10] Njira zonse za Yehova ndi zachikondi ndi zokhulupirika kwa iwo amene amasunga zofuna za pangano lake.

[11] Chifukwa cha dzina lanu, Inu Yehova, khululukireni mphulupulu zanga, ngakhale kuti ndi zochuluka.

[12] Tsono ndani munthu amene amaopa Yehova? Yehova adzamulangiza njira yoti ayitsate.

[13] Iye adzakhala pa ulemerero masiku ake onse, ndipo zidzukulu zake zidzalandira dziko ngati cholowa chawo.

[14] Yehova amawulula chinsinsi chake kwa iwo amene amamuopa; amawulula pangano lake kwa iwowo.

[15] Maso anga ali pa Yehova nthawi zonse, pakuti ndi Iye yekha amene adzawonjola mapazi anga mu msampha.

[16] Tembenukirani kwa ine ndipo mundikomere mtima, pakuti ndili ndekhandekha ndipo ndikuzunzika.

[17] Masautso a mu mtima mwanga achulukirachulukira; masuleni ku zowawa zanga.

[18] Penyani mazunzo anga ndi zovuta zanga ndipo mufafanize machimo anga onse.

[19] Onani mmene adani anga achulukira ndi momwe chidani chawo ndi ine chakulira.

[20] Tetezani moyo wanga ndi kundilanditsa; musalole kuti ndichite manyazi, pakuti ndimathawira kwa Inu.

[21] Kukhulupirika ndi kulungama kwanga kunditeteze, chifukwa chiyembekezo changa chili mwa Inu.

[22] Wombolani Israeli Inu Mulungu, ku mavuto ake onse!

Masalimo — Chapters