Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 0:55

[1] Ndikweza maso anga ku mapiri; kodi thandizo langa limachokera kuti?

[2] Thandizo langa limachokera kwa Yehova, wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.

[3] Sadzalola kuti phazi lako literereke; Iye amene amakusunga sadzawodzera.

[4] Taonani, Iye amene amasunga Israeli sadzawodzera kapena kugona.

[5] Yehova ndiye amene amakusunga; Yehova ndiye mthunzi wako ku dzanja lako lamanja.

[6] Dzuwa silidzakupweteka nthawi ya masana, kapena mwezi nthawi ya usiku.

[7] Yehova adzakuteteza ku zoyipa zonse; adzasunga moyo wako.

[8] Yehova adzayangʼanira kutuluka kwako ndi kulowa kwako; kuyambira tsopano mpaka muyaya.

Masalimo — Chapters