Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:42

[1] Atamandike Yehova Thanthwe langa, amene amaphunzitsa manja anga kuchita nkhondo; zala zanga kumenya nkhondo.

[2] Iye ndiye Mulungu wanga wachikondi ndi malo anga otetezedwa, linga langa ndi mpulumutsi wanga, chishango changa mmene ine ndimathawiramo, amene amagonjetsa mitundu ya anthu pansi panga.

[3] Inu Yehova, munthu nʼchiyani kuti mumamusamalira, mwana wa munthu kuti muzimuganizira?

[4] Munthu ali ngati mpweya; masiku ake ali ngati mthunzi wosakhalitsa.

[5] Ngʼambani mayiko akumwamba, Inu Yehova, ndipo tsikani pansi; khudzani mapiri kuti atulutse utsi.

[6] Tumizani zingʼaningʼani ndi kubalalitsa adani; ponyani mivi yanu ndi kuwathamangitsa.

[7] Tambasulani dzanja lanu kuchokera kumwamba; landitseni ndi kundipulumutsa, ku madzi amphamvu, mʼmanja mwa anthu achilendo,

[8] amene pakamwa pawo ndi podzala ndi mabodza, amene dzanja lawo lamanja ndi lachinyengo.

[9] Ndidzakuyimbirani nyimbo yatsopano Inu Mulungu; ndidzakuyimbirani nyimbo pa zeze wa nsambo khumi,

[10] kwa Iye amene amapambanitsa mafumu, amene amapulumutsa Davide mtumiki wake ku lupanga loopsa.

[11] Landitseni ndi kundipulumutsa, mʼmanja mwa anthu achilendo, amene pakamwa pawo ndi podzaza ndi mabodza, amene dzanja lawo lamanja ndi lachinyengo.

[12] Ndipo ana aamuna pa chinyamata chawo adzakhala ngati mbewu yosamalidwa bwino, ana athu aakazi adzakhala ngati zipilala zosemedwa bwino, zokongoletsera nyumba yaufumu.

[13] Nkhokwe zathu zidzakhala zodzaza ndi zokolola za mtundu uliwonse. Nkhosa zathu zidzaswana miyandamiyanda pa mabusa athu.

[14] Ngʼombe zathu zidzanyamula katundu wolemera. Sipadzakhala mingʼalu pa makoma, sipadzakhalanso kupita ku ukapolo, mʼmisewu mwathu simudzakhala kulira chifukwa cha mavuto.

[15] Odala anthu amene adzalandira madalitso awa; odala anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.

Masalimo — Chapters