Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:24

[1] Ndiyankheni pamene ndiyitana Inu, Inu Mulungu wa chilungamo changa. Pumulitseni ku zowawa zanga; chitireni chifundo ndi kumva pemphero langa.

[2] Anthu inu, mpaka liti mudzakhala mukusandutsa ulemerero wanga kukhala manyazi? Mpaka liti mudzakonda zachabe ndi kufuna milungu yabodza? q4 Sela.

[3] Dziwani kuti Yehova wadziyikira padera anthu okhulupirika; Yehova adzamva pamene ndidzamuyitana.

[4] Kwiyani koma musachimwe; pamene muli pa mabedi anu, santhulani mitima yanu ndi kukhala chete. q4 Sela

[5] Perekani nsembe zolungama ndipo dalirani Yehova.

[6] Ambiri akufunsa kuti, “Ndani angationetse chabwino chilichonse?” Kuwunika kwa nkhope yanu kutiwalire, Inu Yehova.

[7] Inu mwadzaza mtima wanga ndi chimwemwe chachikulu kuposa kuchuluka kwa tirigu wawo ndi vinyo watsopano.

[8] Ine ndidzagona ndi kupeza tulo mwamtendere, pakuti Inu nokha, Inu Yehova, mumandisamalira bwino.

Masalimo — Chapters