[1] Ndimakonda Yehova pakuti Iyeyo amamva mawu anga; Iye amamva kulira kwanga kopempha chifundo.
[2] Pakuti ananditchera khutu, ndidzayitana Iye masiku onse a moyo wanga.
[3] Zingwe za imfa zinandizinga, zoopsa za ku dziko la anthu akufa zinandigwera; ndinapeza mavuto ndi chisoni.
[4] Pamenepo ndinayitana dzina la Yehova: “Inu Yehova, pulumutseni!”
[5] Yehova ndi wokoma mtima ndi wolungama Mulungu wathu ndi wodzaza ndi chifundo.
[6] Yehova amateteza munthu wodzichepetsa mtima; pamene ndinali ndi chosowa chachikulu, Iye anandipulumutsa.
[7] Pumula iwe moyo wanga, pakuti Yehova wakuchitira zokoma.
[8] Pakuti Inu Yehova mwapulumutsa moyo wanga ku imfa, maso anga ku misozi, mapazi anga kuti angapunthwe,
[9] kuti ine ndiyende pamaso pa Yehova mʼdziko la anthu amoyo.
[10] Ine ndinakhulupirira; choncho ndinati, “Ndasautsidwa kwambiri.”
[11] Ndipo ndili mʼnkhawa yanga ndinati, “Anthu onse ndi abodza.”
[12] Ndingamubwezere chiyani Yehova, chifukwa cha zokoma zake zonse zimene wandichitira?
[13] Ndidzakweza chikho cha chipulumutso ndipo ndidzayitana dzina la Yehova.
[14] Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova pamaso pa anthu ake onse.
[15] Imfa ya anthu oyera mtima ndi yamtengowapatali pamaso pa Yehova.
[16] Inu Yehova, zoonadi ndine mtumiki wanu: ndine mtumiki wanu, mwana wa mdzakazi wanu; Inu mwamasula maunyolo anga.
[17] Ndidzapereka nsembe yachiyamiko kwa Inu ndipo ndidzayitanira pa dzina la Yehova.
[18] Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova pamaso pa anthu ake onse,
[19] mʼmabwalo a nyumba ya Yehova, mʼkati mwako iwe Yerusalemu. Tamandani Yehova.