[1] Inu Yehova, mfumu ikusangalala mu mphamvu yanu, chimwemwe chake nʼchachikuludi pa kupambana kumene mumapereka!
[2] Inu mwayipatsa zokhumba za mtima wake ndipo simunayimane zopempha za pa milomo yake. q4 Sela
[3] Inu munayilandira ndi madalitso ochuluka ndipo munayiveka chipewa chaufumu chagolide weniweni pa mutu wake.
[4] Iye anakupemphani moyo, ndipo munamupatsa masiku ochuluka kwamuyaya.
[5] Kudzera mʼzigonjetso zimene munapereka, ulemerero wake ndi waukulu; Inu mwapereka pa iyo ulemerero ndi ufumu.
[6] Zoonadi Inu mwayipatsa madalitso amuyaya, Inu mwayipatsa chisangalalo ndi chimwemwe chimene chili pamaso panu.
[7] Pakuti mfumu imadalira Yehova; kudzera mʼchikondi chake chosatha cha Wammwambamwamba, iyo sidzagwedezeka.
[8] Dzanja lanu lidzayimitsa adani anu onse; dzanja lanu lamanja lidzagwira adani anu.
[9] Pa nthawi ya kuonekera kwanu mudzawasandutsa ngʼanjo yamoto yotentha. Mu ukali wake Yehova adzawameza, ndipo moto wake udzawatha.
[10] Inu mudzawononga ana awo pa dziko lapansi, zidzukulu zawo pakati pa anthu.
[11] Ngakhale iwo akukonzereni chiwembu mwa kuchenjera kwawo sadzapambana;
[12] pakuti mudzawapirikitsa ndipo adzaonetsa misana yawo pamene mudzawaloza ndi mivi yanu.
[13] Mukwezeke Inu Yehova mʼmphamvu yanu, ife tidzayimba nyimbo ndi kutamanda mphamvu yanu.