Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:54

[1] Tamandani Yehova. Tamandani dzina la Yehova; mutamandeni, inu atumiki a Yehova,

[2] amene mumatumikira mʼnyumba ya Yehova, mʼmabwalo a nyumba ya Mulungu wathu.

[3] Tamandani Yehova, pakuti Yehova ndi wabwino; imbani nyimbo zotamanda dzina lake, pakuti nʼkokoma kutero,

[4] Pakuti Yehova wasankha Yakobo kuti akhale wake, Israeli kuti akhale chuma chake chapamtima.

[5] Ndikudziwa kuti Yehova ndi wamkulu, kuti Ambuye athu ndi wamkulu kuposa milungu yonse.

[6] Yehova amachita chilichonse chimene chimamukomera, kumwamba ndi dziko lapansi, ku nyanja zazikulu ndi ku malo ake onse akuya.

[7] Iye amatulutsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi, amatumiza zingʼaningʼani pamodzi ndi mvula ndipo amatulutsa mphepo ku malo ake osungiramo.

[8] Anakantha ana oyamba kubadwa a Igupto, ana oyamba kubadwa a anthu ndi nyama.

[9] Iye anatumiza zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa pakati pako, iwe Igupto, kutsutsana ndi Farao pamodzi ndi atumiki ake onse.

[10] Iye anakantha mitundu yambiri ya anthu ndi kupha mafumu amphamvu:

[11] Sihoni mfumu ya Aamori, Ogi mfumu ya Basani, ndi maufumu onse a ku Kanaani;

[12] ndipo anapereka dziko lawo ngati cholowa, cholowa cha anthu ake Aisraeli.

[13] Dzina lanu, Inu Yehova, ndi losatha mpaka muyaya, mbiri yanu, Inu Yehova, idziwika mibado yonse.

[14] Pakuti Yehova adzaonetsa kuti anthu ake ngosalakwa, ndipo adzachitira chifundo atumiki ake.

[15] Mafano a mitundu ya anthu ndi siliva ndi golide, opangidwa ndi manja a anthu.

[16] Pakamwa ali napo koma sayankhula maso ali nawo, koma sapenya;

[17] makutu ali nawo, koma sakumva ndipo mʼkamwa mwawo mulibe mpweya uliwonse.

[18] Iwo amene amapanga mafanowo adzakhala ngati mafanowo, chimodzimodzinso iwo amene amadalira mafanowo.

[19] Inu nyumba ya Israeli, tamandani Yehova; inu nyumba ya Aaroni, tamandani Yehova;

[20] Inu nyumba ya Levi, tamandani Yehova; Inu amene mumaopa Iye, tamandani Yehova.

[21] Wodalitsika ndi Yehova kuchokera mʼZiyoni, amene amakhala mu Yerusalemu. Tamandani Yehova.

Masalimo — Chapters