Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:50

[1] Mulungu amadziwika mu Yuda; dzina lake ndi lotchuka mu Israeli.

[2] Tenti yake ili mu Salemu, malo ake okhalamo mu Ziyoni.

[3] Kumeneko Iye anathyola mivi yowuluka, zishango ndi malupanga, zida zankhondo. q4 Sela

[4] Wolemekezeka ndinu, wamphamvu kuposa mapiri amene ali ndi nyama zambiri.

[5] Anthu owuma mtima amagona atalandidwa chuma, Iwowo amagona tulo tawo totsiriza; palibe mmodzi wamphamvu amene angatukule manja ake.

[6] Pa kudzudzula kwanu, Inu Mulungu wa Yakobo, kavalo pamodzi ndi galeta zimakhala chete zitagona pansi.

[7] Inu nokha ndiye muyenera kuopedwa. Angathe kuyima pamaso panu ndani mukakwiya?

[8] Kuchokera kumwamba Inu munalengeza chiweruzo, ndipo dziko linaopa ndi kukhala chete,

[9] pamene Inu Mulungu munadzuka kuti muweruze, kupulumutsa onse osautsidwa mʼdziko. q4 Sela

[10] Zoonadi, ukali wanu pa anthu umakubweretserani matamando ndipo opulumuka ku ukali wanu mumawasunga pafupi nanu.

[11] Chitani malumbiro kwa Yehova Mulungu wanu ndipo muwakwaniritse; anthu onse omuzungulira abweretse mphatso kwa Iye amene ayenera kuopedwa.

[12] Iye amaswa mzimu wa olamulira; amaopedwa ndi mafumu a dziko lapansi.

Masalimo — Chapters