Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:46

[1] Tcherani khutu Inu mʼbusa wa Israeli, Inu amene mumatsogolera Yosefe monga nkhosa; Inu amene mumakhala pa mpando waufumu pakati pa akerubi, walani

[2] kwa Efereimu, Benjamini ndi Manase. Utsani mphamvu yanu; bwerani ndi kutipulumutsa.

[3] Tibwezereni mwakale Inu Mulungu; nkhope yanu itiwalire kuti tipulumutsidwe.

[4] Inu Mulungu Wamphamvuzonse, mpaka liti mkwiyo wanu udzanyeka kutsutsana ndi mapemphero a anthu anu?

[5] Mwawadyetsa buledi wa misozi; mwachitisa iwo kumwa misozi yodzaza mbale.

[6] Mwachititsa kuti tikhale gwero la mikangano pakati pa anansi athu, ndipo adani athu akutinyoza.

[7] Tibwezereni mwakale Inu Mulungu Wamphamvuzonse, nkhope yanu itiwalire kuti tipulumutsidwe.

[8] Munatulutsa mpesa kuchoka ku Igupto; munathamangitsa anthu a mitundu ina ndi kuwudzala mpesawo.

[9] Munawulimira munda wamphesawo, ndipo unamera ndi kudzaza dziko.

[10] Mapiri anaphimbidwa ndi mthunzi wake, mikungudza yamphamvu ndi nthambi zake.

[11] Unatambalitsa nthambi zake mpaka ku nyanja, mphukira zake mpaka ku mtsinje.

[12] Chifukwa chiyani mwagwetsa makoma ake kuti onse amene akudutsa athyole mphesa zake?

[13] Nguluwe zochokera mʼnkhalango zikuwononga ndipo zirombo za mthengo zimawudya.

[14] Bweraninso kwa ife Inu Mulungu Wamphamvuzonse! Yangʼanani pansi muli kumwambako ndipo muone! Uyangʼanireni mpesa umenewu,

[15] muzu umene dzanja lanu lamanja ladzala, mwana amene inu munamukuza nokha.

[16] Mpesa wanu wadulidwa ndi kutenthedwa ndi moto; pakudzudzula kwanu anthu anu awonongeka.

[17] Dzanja lanu likhale pa munthu amene ali ku dzanja lanu lamanja, mwana wa munthu amene mwalera nokha.

[18] Ndipo ife sitidzatembenukira kumbali kuchoka kwa Inu; titsitsimutseni ndipo tidzayitana pa dzina lanu.

[19] Tibwezereni mwakale Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse nkhope yanu itiwalire kuti tipulumutsidwe.

Masalimo — Chapters