[1] Inu Yehova, mulimbane nawo amene akulimbana nane; mumenyane nawo amene akumenyana nane.
[2] Tengani chishango ndi lihawo; dzukani ndipo bwerani mundithandize.
[3] Tengani mkondo ndi nthungo, kulimbana ndi iwo amene akundithamangitsa. Uzani moyo wanga kuti, “Ine ndine chipulumutso chako.”
[4] Iwo amene akufunafuna moyo wanga anyozedwe ndi kuchita manyazi; iwo amene akukonza kuti moyo wanga uwonongeke abwerere mʼmbuyo mochititsa mantha.
[5] Akhale ngati mankhusu owuluka ndi mphepo pamene mngelo wa Yehova akuwapirikitsa.
[6] Njira yawo ikhale ya mdima ndi yoterera pamene mngelo wa Yehova akuwathamangitsa.
[7] Popeza ananditchera ukonde popanda chifukwa ndipo popanda chifukwa andikumbira dzenje,
[8] chiwonongeko chiwapeza modzidzimutsa ukonde umene iwo abisa uwakole, agwere mʼdzenje kuti awonongedwe.
[9] Pamenepo moyo wanga udzakondwera mwa Yehova ndi kusangalala ndi chipulumutso chake.
[10] Thupi langa lidzafuwula mokondwera, “Ndani angafanane nanu Yehova? Mumalanditsa osauka kwa amene ali ndi mphamvu zambiri, osauka ndi osowa kwa iwo amene amawalanda.”
[11] Mboni zopanda chisoni zinayimirira, zinandifunsa zinthu zimene sindikuzidziwa.
[12] Iwo anandibwezera zoyipa pa zabwino ndipo anasiya moyo wanga pa chisoni.
[13] Koma pamene iwo ankadwala, ine ndinavala chiguduli ndi kudzichepetsa ndekha posala zakudya. Pamene mapemphero anga anabwerera kwa ine osayankhidwa,
[14] ndinayendayenda ndi kulira maliro, kumulira ngati bwenzi langa kapena mʼbale wanga. Ndinaweramitsa mutu wanga mosweka mtima kukhala ngati ndikulira amayi anga.
[15] Koma pamene ndinaphunthwa, iwo anasonkhana mosangalala; ondithira nkhondo anasonkhana kutsutsana nane, ineyo osadziwa. Iwo sanasiye kundiyankhulira mawu onyoza.
[16] Monga anthu osapembedza, iwo anandinyoza mwachipongwe; anandikukutira mano awo.
[17] Ambuye, mpaka liti mudzakhala mukungoyangʼana? Landitsani moyo wanga ku chiwonongeko chawo, moyo wanga wopambana ku mikango.
[18] Ndidzakuyamikani mu msonkhano waukulu; pakati pa gulu lalikulu la anthu ndidzakutamandani.
[19] Musalole adani anga onyenga akondwere chifukwa cha masautso anga; musalole kuti amene amadana nane popanda chifukwa andiyangʼane chamʼmbali mondinyoza.
[20] Iwowo sayankhula mwamtendere, koma amaganizira zonamizira iwo amene amakhala mwabata mʼdziko.
[21] Iwo amandiseka mofuwula ndipo amati, “Haa! Haa! Ndipo ndi maso athuwa ife taziona.”
[22] Yehova mwaona zimenezi; musakhale chete. Ambuye musakhale kutali ndi ine.
[23] Dzukani, ndipo nyamukani kunditeteza! Mulimbane nawo chifukwa cha ine, Mulungu wanga ndi Ambuye anga.
[24] Onetsani kusalakwa kwanga mwa chilungamo chanu, Inu Yehova Mulungu wanga. Musalole kuti akondwere chifukwa cha mavuto anga.
[25] Musalole kuti aganize kuti, “Amati atani, zachitika monga momwe timafunira!” Kapena kunena kuti, “Tamutha ameneyu basi.”
[26] Onse amene amakondwera ndi masautso anga achite manyazi ndi kusokonezeka. Onse amene amadzikweza kufuna kundipambana, avekedwe manyazi ndi mnyozo ngati zovala.
[27] Koma amene amakondwera chifukwa chakuti ndine wosalakwa, afuwule mwachimwemwe ndi chisangalalo. Nthawi zonse azinena kuti, “Yehova akwezeke, Iye amene amakondwera ndi kupeza bwino kwa mtumiki wake.”
[28] Pakamwa panga padzayankhula za chilungamo chanu ndi za matamando anu tsiku lonse.