[1] Mulungu wanga, Mulungu wanga, nʼchifukwa chiyani mwandisiya? Chifuwa chiyani simukundithandiza ndi pangʼono pomwe? Nʼchifukwa chiyani simukumva mawu a kudandaula kwanga?
[2] Inu Mulungu wanga, ine ndimalira masana, koma simuyankha, usikunso, ndipo sindikhala chete.
[3] Inu ndinu Woyera, wokhala pa mpando waufumu; ndinu matamando a Israeli.
[4] Pa inu makolo athu anadalira; iwo anadalira ndipo Inu munawapulumutsa.
[5] Analirira kwa inu ndipo munawapulumutsa. Iwo anakhulupirira Inu ndipo simunawakhumudwitse.
[6] Koma ine ndine nyongolotsi osati munthu, wosekedwa ndi wonyozedwa ndi anthu onse.
[7] Onse amene amandiona amandiseka; amandiyankhulira mawu achipongwe akupukusa mitu yawo kunena kuti
[8] “Iyeyu amadalira Yehova, musiyeni Yehovayo amulanditse. Musiyeni Yehova amupulumutse popeza amakondwera mwa Yehovayo.”
[9] Komabe Inu ndinu amene munandibadwitsa, munanditulutsa mʼmimba mwa amayi anga. Munachititsa kuti ndizikudalirani ngakhale pa nthawi imene ndinkayamwa.
[10] Chibadwire ine ndinaperekedwa kwa Inu; kuchokera mʼmimba mwa amayi anga Inu mwakhala muli Mulungu wanga.
[11] Musakhale kutali ndi ine, pakuti mavuto ali pafupi ndipo palibe wina wondipulumutsa.
[12] Ngʼombe zazimuna zandizungulira; ngʼombe zazimuna zamphamvu za ku Basani zandizinga.
[13] Mikango yobangula pokadzula nyama, yatsekula kwambiri pakamwa pawo kulimbana nane.
[14] Ine ndatayika pansi ngati madzi ndipo mafupa anga onse achoka mʼmalo mwake. Mtima wanga wasanduka phula; wasungunuka mʼkati mwanga.
[15] Mphamvu zanga zauma ngati phale, ndipo lilime langa lamamatira ku nsagwada; mwandigoneka mʼfumbi la imfa.
[16] Agalu andizungulira; gulu la anthu oyipa landizinga. Alasa manja ndi mapazi anga.
[17] Ine nditha kuwerenga mafupa anga onse; anthu amandiyangʼanitsitsa ndi kundidzuma.
[18] Iwo agawana zovala zanga pakati pawo ndi kuchita maere pa zovala zangazo.
[19] Koma Inu Yehova, musakhale kutali; Inu mphamvu yanga, bwerani msanga kuti mudzandithandize.
[20] Pulumutsani moyo wanga ku lupanga, moyo wanga wopambanawu ku mphamvu ya agalu.
[21] Ndilanditseni mʼkamwa mwa mikango; pulumutseni ku nyanga za njati.
[22] Ine ndidzalengeza dzina lanu kwa abale anga; ndidzakutamandani mu msonkhano.
[23] Inu amene mumaopa Yehova mutamandeni! Inu zidzukulu zonse za Yakobo, mulemekezeni! Muopeni mwaulemu, inu zidzukulu zonse za Israeli!
[24] Pakuti Iye sanapeputse kapena kunyoza kuvutika kwa wosautsidwayo; Iye sanabise nkhope yake kwa iye. Koma anamvera kulira kwake kofuna thandizo.
[25] Ndidzakutamandani pa msonkhano waukulu chifukwa cha zimene mwandichitira. Ndidzakwaniritsa lonjezo langa pamaso pa amene amaopa Inu.
[26] Osauka adzadya ndipo adzakhuta; iwo amene amafunafuna Yehova adzamutamanda. Mitima yanu ikhale ndi moyo mpaka muyaya!
[27] Malekezero onse a dziko lapansi adzakumbukira Yehova ndi kutembenukira kwa Iye, ndipo mabanja a mitundu ya anthu adzawerama pamaso pake,
[28] pakuti ulamuliro ndi wake wa Yehova ndipo Iye amalamulira anthu a mitundu yonse.
[29] Anthu olemera onse a dziko lapansi adzachita phwando ndi kulambira; onse amene amapita ku fumbi adzagwada pamaso pake; iwo amene sangathe kudzisunga okha ndi moyo.
[30] Zidzukulu zamʼtsogolo zidzamutumikira Iye; mibado ya mʼtsogolo idzawuzidwa za Ambuye.
[31] Iwo adzalengeza za chilungamo chake kwa anthu amene pano sanabadwe pakuti Iye wachita zimenezi.