Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:05

[1] Tamandani Yehova. Tamandani Yehova, inu a kumwamba, mutamandeni Iye, inu a mlengalenga.

[2] Mutamandeni, inu angelo ake onse, mutamandeni, mutamandeni, inu zolengedwa za mmwamba.

[3] Mutamandeni, inu dzuwa ndi mwezi, mutamandeni, inu nonse nyenyezi zowala.

[4] Mutamandeni, inu thambo la kumwambamwamba ndi inu madzi a pamwamba pa thambo.

[5] Zonse zitamande dzina la Yehova pakuti Iye analamula ndipo zinalengedwa.

[6] Iye anaziyika pa malo ake ku nthawi za nthawi; analamula ndipo sizidzatha.

[7] Tamandani Yehova pa dziko lapansi, inu zolengedwa zikuluzikulu za mʼnyanja, ndi nyanja zonse zakuya,

[8] inu zingʼaningʼani ndi matalala, chipale ndi mitambo, mphepo yamkuntho imene imakwaniritsa mawu ake,

[9] inu mapiri ndi zitunda zonse, inu mitengo ya zipatso ndi mikungudza yonse,

[10] inu nyama zakuthengo ndi ngʼombe zonse, inu zolengedwa zingʼonozingʼono ndi mbalame zowuluka.

[11] Inu mafumu a dziko lapansi ndi anthu a mitundu yonse, inu akalonga ndi olamulira a dziko lapansi.

[12] Inu anyamata ndi anamwali, inu nkhalamba ndi ana omwe.

[13] Onsewo atamande dzina la Yehova pakuti dzina lake lokha ndi lolemekezeka; ulemerero wake ndi woopsa pa dziko lapansi pano ndi kumwamba komwe.

[14] Iye wakwezera nyanga anthu ake, matamando a anthu ake onse oyera mtima, Aisraeli, anthu a pamtima pake. Tamandani Yehova.

Masalimo — Chapters