Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:09

[1] Tamandani Yehova. Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, matamando ake mu msonkhano wa oyera mtima.

[2] Israeli asangalale mwa mlengi wake; anthu a ku Ziyoni akondwere mwa Mfumu yawo.

[3] Atamande dzina lake povina ndi kuyimbira Iye nyimbo ndi tambolini ndi pangwe.

[4] Pakuti Yehova amakondwera ndi anthu ake; Iye amaveka chipulumutso odzichepetsa.

[5] Oyera mtima asangalale mu ulemu wake ndi kuyimba mwachimwemwe pa mabedi awo.

[6] Matamando a Mulungu akhale pakamwa pawo, ndi lupanga lakuthwa konsekonse mʼmanja mwawo,

[7] kubwezera chilango anthu a mitundu ina, ndi kulanga anthu a mitundu yonse,

[8] kumanga mafumu awo ndi zingwe, anthu awo otchuka ndi unyolo wachitsulo,

[9] kuchita zimene zinalembedwa zotsutsana nawo Uwu ndi ulemerero wa oyera mtima ake onse. Tamandani Yehova.

Masalimo — Chapters