[1] Tamandani Yehova. Nʼkwabwino kwambiri kuyimba nyimbo zamatamando kwa Mulungu wathu, nʼkokondweretsa ndi koyenera kumutamanda!
[2] Yehova akumanga Yerusalemu; Iye akusonkhanitsa amʼndende a Israeli.
[3] Akutsogolera anthu osweka mtima ndi kumanga mabala awo.
[4] Amadziwa chiwerengero cha nyenyezi, ndipo iliyonse amayitchula dzina.
[5] Yehova ndi wamkulu ndi wamphamvu kwambiri; nzeru zake zilibe malire.
[6] Yehova amagwiriziza anthu odzichepetsa, koma amagwetsa pansi anthu oyipa.
[7] Imbirani Yehova ndi mayamiko; imbani nyimbo kwa Mulungu ndi pangwe.
[8] Iye amaphimba mlengalenga ndi mitambo; amapereka mvula ku dziko lapansi ndi kumeretsa udzu mʼmapiri.
[9] Iye amapereka chakudya kwa ngʼombe ndi kwa ana a makwangwala pamene akulira chakudya.
[10] Chikondwerero chake sichili mʼmphamvu za kavalo, kapena mʼmiyendo ya anthu amphamvu.
[11] Yehova amakondwera ndi amene amamuopa, amene chiyembekezo chawo chili mʼchikondi chake chosasinthika.
[12] Lemekeza Yehova, iwe Yerusalemu; tamanda Mulungu wako, iwe Ziyoni,
[13] pakuti Iye amalimbitsa mipiringidzo ya zipata zako ndi kudalitsa anthu ako mwa iwe.
[14] Iye amabweretsa mtendere mʼmalire mwako ndi kukukhutitsa ndi ufa wa tirigu wosalala.
[15] Iyeyo amapereka lamulo pa dziko lapansi; mawu ake amayenda mwaliwiro.
[16] Amagwetsa chisanu ngati ubweya ndi kumwaza chipale ngati phulusa.
[17] Amagwetsa matalala ngati miyala. Kodi ndani angathe kupirira kuzizira kwake?
[18] Amatumiza mawu ake ndipo chisanucho chimasungunuka; amawombetsa mphepo ndipo madzi amayenda.
[19] Iye anawulula mawu ake kwa Yakobo, malamulo ake ndi zophunzitsa zake kwa Israeli.
[20] Sanachitepo zimenezi kwa mtundu wina uliwonse wa anthu; anthu enawo sadziwa malamulo ake. Tamandani Yehova.