Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:07

[1] Imvani izi anthu a mitundu yonse; mvetserani, nonse amene mumakhala pa dziko lonse,

[2] anthu wamba pamodzi ndi anthu odziwika, olemera pamodzinso ndi osauka:

[3] Pakamwa panga padzayankhula mawu anzeru; mawu ochokera mu mtima mwanga adzapereka nzeru.

[4] Ndidzatchera khutu langa ku mwambo, ndi pangwe ndidzafotokoza momveka mwambi wanga.

[5] Ine ndichitirenji mantha pamene masiku oyipa afika, pamene achinyengo oyipa andizungulira.

[6] Iwo amene adalira kulemera kwawo ndi kutamandira kuchuluka kwa chuma chawo?

[7] Palibe munthu amene angawombole moyo wa mnzake kapena kuperekera mnzake dipo kwa Mulungu.

[8] Dipo la moyo ndi la mtengowapatali, palibe malipiro amene angakwanire,

[9] kuti iye akhale ndi moyo mpaka muyaya ndi kusapita ku manda.

[10] Pakuti onse amaona kuti anthu anzeru amamwalira; opusa ndi opanda nzeru chimodzimodzinso amawonongeka ndipo amasiyira chuma chawo anthu ena.

[11] Manda awo adzakhala nyumba zawo mpaka muyaya, malo awo okhalako kwa nthawi yonse ya mibado yawo, ngakhale anatchula malo mayina awo.

[12] Ngakhale munthu akhale wachuma chotani, adzafa ngati nyama.

[13] Izi ndi zimene zimachitikira iwo amene amadzidalira okha, ndi owatsatira awo amene amavomereza zimene amayankhula. q4 Sela

[14] Monga nkhosa iwo ayenera kupita ku manda, ndipo imfa idzawadya. Olungama adzawalamulira mmawa; matupi awo adzavunda mʼmanda, kutali ndi nyumba zawo zaufumu.

[15] Koma Mulungu adzawombola moyo wanga kuchoka ku manda; ndithu Iye adzanditengera kwa Iye mwini.

[16] Usavutike mu mtima pamene munthu akulemera, pamene ulemerero wa nyumba yake ukuchulukirachulukira;

[17] Pakuti sadzatenga kanthu pamodzi naye pamene wamwalira, ulemerero wake sudzapita pamodzi naye.

[18] Ngakhale pamene munthuyo ali moyo amadziyesa wodala, ndipo ngakhale atamandidwe pamene zinthu zikumuyendera bwino,

[19] iyeyo adzakakhala pamodzi ndi mʼbado wa makolo ake, amene sadzaonanso kuwala.

[20] Munthu amene ali ndi chuma koma wopanda nzeru adzafa ngati nyama yakuthengo.

Masalimo — Chapters