Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:00

[1] Yehova atikomere mtima ndi kutidalitsa, achititse kuti nkhope yake itiwalire.

[2] Kuti njira zanu zidziwike pa dziko lapansi, chipulumutso chanu pakati pa mitundu yonse.

[3] Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu; mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.

[4] Mitundu yonse ya anthu isangalale ndi kuyimba mwachimwemwe, pakuti inu mumaweruza mitundu ya anthu mwachilungamo ndi kutsogolera mitundu ya anthu a dziko lapansi.

[5] Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu; mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.

[6] Nthaka yabereka zokolola zake; tidalitseni Mulungu wathu.

[7] Mulungu atidalitse kuti pamenepo malekezero onse a dziko lapansi apembedze Iyeyo.

Masalimo — Chapters