Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 0:58

[1] Pulumutseni Inu Mulungu, mwa dzina lanu; onetsani kuti ndine wosalakwa mwamphamvu yanu.

[2] Imvani pemphero langa, Inu Mulungu mvetserani mawu a pakamwa panga.

[3] Alendo akundithira nkhondo; anthu ankhanza akufunafuna moyo wanga, anthu amene salabadira za Mulungu.

[4] Zoonadi Mulungu ndi thandizo langa; Ambuye ndiye amene amandichirikiza ine.

[5] Lolani kuti choyipa chifike pa iwo amene amandichita chipongwe; mwa kukhulupirika kwanu awonongeni.

[6] Ine ndidzapereka nsembe yaufulu kwa Inu; ndidzatamanda dzina lanu, Inu Yehova, pakuti ndi labwino.

[7] Pakuti Iyeyo wandipulumutsa ku masautso anga onse, ndipo maso anga apenya kupambana kwa pa adani anga.

Masalimo — Chapters