Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:51

[1] Ndidzakukwezani Yehova, chifukwa mwanditulutsa kwakuya, ndipo simunalole kuti adani anga akondwere pa ine.

[2] Inu Yehova Mulungu wanga ndinapempha kwa Inu thandizo ndipo Inu munandichiritsa.

[3] Inu Yehova, munanditulutsa ku manda, munandisunga kuti ndisatsalire mʼdzenje.

[4] Imbirani Yehova inu anthu ake okhulupirika; tamandani dzina lake loyera.

[5] Pakuti mkwiyo wake umakhala kwa kanthawi koma kukoma mtima kwake ndi kwa moyo wonse; utha kuchezera kulira usiku wonse, koma chimwemwe chimabwera mmawa.

[6] Pamene ndinaona kuti ndili otetezedwa ndinati, “Sindidzagwedezekanso.”

[7] Inu Yehova, pamene munandikomera mtima, munachititsa phiri langa kuyima chilili; koma pamene munabisa nkhope yanu, ndinataya mtima.

[8] Kwa Inu Yehova ndinayitana; kwa Ambuye ndinapempha chifundo;

[9] “Kodi pali phindu lanji powonongeka kwanga ngati nditsikira ku dzenje? Kodi fumbi lidzakutamandani Inu? Kodi lidzalengeza za kukhulupirika kwanu?

[10] Imvani Yehova ndipo mundichitire chifundo; Yehova mukhale thandizo langa.”

[11] Inu munasandutsa kulira kwanga kukhala kuvina; munachotsa chiguduli changa ndi kundiveka ndi chimwemwe,

[12] kuti mtima wanga uthe kuyimbira Inu usakhale chete. Yehova Mulungu wanga, ndidzapereka kwa Inu mayamiko kwamuyaya.

Masalimo — Chapters