Listen to this chapter • 1:02
[1] Yehova ndiye mʼbusa wanga, sindidzasowa kanthu.
[2] Amandigoneka pa msipu wobiriwira, amanditsogolera ku madzi akumwa abwino,
[3] amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera mʼnjira zachilungamo chifukwa cha dzina lake.
[4] Ngakhale ndiyende mʼchigwa cha mdima wakuda bii, sindidzaopa choyipa, pakuti Inu muli ndi ine; chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditonthoza.
[5] Mumandikonzera chakudya adani anga akuona. Mumadzoza mutu wanga ndi mafuta; chikho changa chimasefukira.
[6] Zoonadi, zokoma ndi chikondi chosasinthika zidzanditsata masiku onse a moyo wanga, ndipo ndidzakhala mʼNyumba ya Yehova kwamuyaya.
Masalimo — Chapters
11:1922:0331:1341:2452:2361:3273:0081:3193:14103:14111:16121:21130:58141:23151:09161:43172:42187:48192:28201:25212:07225:05231:02241:40253:15261:46272:45281:56291:33301:51314:09322:00333:03342:59354:52362:01375:50382:40392:29403:14411:58422:23431:13443:50453:05461:40471:20482:15493:07503:29513:10521:51531:29540:58553:52562:04572:05581:57592:49602:09611:14622:08631:40641:42652:25662:57671:00686:20695:39700:58713:58723:22733:48743:45751:35761:50772:567810:16792:20802:46812:22821:02832:25842:05851:47862:28871:04882:30897:35902:41912:24922:06930:58943:22951:44962:05971:52981:32991:411000:501011:281023:511033:001045:071056:061066:441076:031082:071094:241101:201111:321121:351131:081141:011152:131162:241170:211183:2711920:011200:501210:551221:111230:471240:511250:541260:551270:571280:491290:581301:091310:411322:351330:381340:251352:541363:271371:311381:231393:271402:061411:441421:131432:041442:421452:571461:281472:311482:051491:091500:54