Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:14

[1] Ine ndidzakutamandani, Inu Yehova, ndi mtima wanga wonse; ndidzafotokoza za zodabwitsa zanu zonse.

[2] Ndidzakondwa ndi kusangalala mwa inu; Ndidzayimba nyimbo zamatamando pa dzina lanu, Inu Wammwambamwamba.

[3] Adani anga amathawa, iwo amapunthwa ndi kuwonongedwa pamaso panu.

[4] Pakuti Inu mwatsimikiza za kulungama kwanga ndi mlandu wanga; Inu mwakhala pa mpando wanu waufumu, kuweruza mwachilungamo.

[5] Mwadzudzula mitundu ya anthu ndipo mwawononga anthu oyipa; Inu mwafafaniza dzina lawo kwamuyaya.

[6] Chiwonongeko chosatha chagwera adani, mwafafaniza mizinda yawo; ngakhale chikumbutso chawo chawonongedwa.

[7] Yehova akulamulira kwamuyaya; wakhazikitsa mpando wake waufumu woweruzira.

[8] Iye adzaweruza dziko mwachilungamo; adzalamulira mitundu ya anthu mosakondera.

[9] Yehova ndiye kothawirako kwa opsinjika mtima, linga pa nthawi ya mavuto.

[10] Iwo amene amadziwa dzina lanu adzadalira Inu, pakuti Inu Yehova, simunawatayepo amene amafunafuna inu.

[11] Imbani nyimbo zamatamando kwa Yehova, ali pa mpando waufumu mu Ziyoni; lengezani pakati pa mitundu ya anthu zimene wachita.

[12] Pakuti Iye amene amabwezera chilango akupha anzawo wakumbukira; Iye salekerera kulira kwa ozunzika.

[13] Inu Yehova, onani momwe adani anga akundizunzira! Chitireni chifundo ndipo ndichotseni pa zipata za imfa,

[14] kuti ndilengeze za matamando anu pa zipata za ana aakazi a Ziyoni, kuti pamenepo ndikondwere ndi chipulumutso chanu.

[15] Mitundu ya anthu yagwa mʼdzenje limene yakumba; mapazi awo akodwa mu ukonde umene anawubisa.

[16] Yehova amadziwika ndi chilungamo chake; oyipa akodwa ndi ntchito za manja awo. q4 Higayoni. Sela

[17] Oyipa amabwerera ku manda, mitundu yonse imene imayiwala Mulungu.

[18] Koma osowa sadzayiwalika nthawi zonse, kapena chiyembekezo cha ozunzika kutayika nthawi zonse.

[19] Dzukani Inu Yehova, musalole munthu kuti apambane; mitundu yonse iweruzidwe pamaso panu.

[20] Akantheni ndi mantha aakulu, Inu Yehova; mitundu idziwe kuti iwo ndi anthu wamba. q4 Sela

Masalimo — Chapters