Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:05

[1] Mtima wanga watakasika ndi nkhani yokoma pamene ndikulakatula mawu anga kwa mfumu; lilime langa ndi cholembera cha wolemba waluso.

[2] Inu ndinu abwino kwambiri kuposa anthu onse ndipo milomo yanu inadzozedwa ndi chikondi cha Mulungu chosasinthika, popeza Mulungu wakudalitsani kwamuyaya.

[3] Mangirirani lupanga lanu mʼchiwuno mwanu, inu munthu wamphamvu; mudziveke nokha ndi ulemerero ndi ukulu wanu.

[4] Mu ukulu wanu mupite mutakwera mwachigonjetso mʼmalo mwa choonadi, kudzichepetsa ndi chilungamo; dzanja lanu lamanja lionetsere ntchito zanu zoopsa.

[5] Mivi yanu yakuthwa ilase mitima ya adani a mfumu, mitundu ya anthu igwe pansi pa mapazi anu.

[6] Mpando wanu waufumu, Inu Mulungu, udzakhala ku nthawi za nthawi; ndodo yaufumu yachilungamo idzakhala ndodo yaufumu ya ufumu wanu.

[7] Inu mumakonda chilungamo ndi kudana ndi zoyipa; choncho Mulungu, Mulungu wanu, wakukhazikani pamwamba pa anzanu pokudzozani ndi mafuta a chimwemwe.

[8] Mikanjo yanu yonse ndi yonunkhira ndi mure ndi aloe ndi kasiya; kuchokera ku nyumba zaufumu zokongoletsedwa ndi mnyanga wanjovu nyimbo za zoyimbira zazingwe zimakusangalatsani.

[9] Ana aakazi a mafumu ali pakati pa akazi anu olemekezeka; ku dzanja lanu lamanja kuli mkwatibwi waufumu ali mu golide wa ku Ofiri.

[10] Tamvera, iwe mwana wa mkazi ganizira ndipo tchera khutu; iwala anthu ako ndi nyumba ya abambo ako.

[11] Mfumu yathedwa nzeru chifukwa cha kukongola kwako; mulemekeze pakuti iyeyo ndiye mbuye wako.

[12] Mwana wa mkazi wa ku Turo adzabwera ndi mphatso, amuna a chuma adzafunafuna kukoma mtima kwako.

[13] Wokongola kwambiri ndi mwana wa mfumu ali mʼchipinda mwake, chovala chake ndi cholukidwa ndi thonje ndi golide.

[14] Atavala zovala zamaluwamaluwa akupita naye kwa mfumu; anamwali okhala naye akumutsatira ndipo abweretsedwa kwa inu.

[15] Iwo akuwaperekeza ndi chimwemwe ndi chisangalalo; akulowa mʼnyumba yaufumu.

[16] Ana ako aamuna adzatenga malo a makolo ako; udzachititsa kuti akhale ana a mfumu mʼdziko lonse.

[17] Ndidzabukitsa mbiri yako mʼmibado yonse; choncho mitundu yonse idzakutamanda ku nthawi za nthawi.

Masalimo — Chapters