[1] Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino; pakuti chikondi chake ndi chosatha.
[2] Owomboledwa a Yehova anene zimenezi amene Iyeyo anawawombola mʼdzanja la mdani,
[3] iwo amene anawasonkhanitsa kuchokera ku mayiko, kuchokera kumadzulo ndi kummawa, kuchokera kumpoto ndi kummwera.
[4] Ena anayendayenda mʼchipululu mopanda kanthu, osapeza njira yopitira ku mzinda kumene akanakakhazikikako.
[5] Iwo anamva njala ndi ludzu, ndipo miyoyo yawo inafowokeratu.
[6] Pamenepo analirira Yehova mʼmavuto awo ndipo Iye anawapulumutsa ku masautso awo.
[7] Iye anawatsogolera mʼnjira yowongoka kupita ku mzinda umene anakakhazikikako.
[8] Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosatha ndi chifukwa cha machitidwe ake odabwitsa kwa anthu onse,
[9] pakuti Iye wapha ludzu la munthu womva ludzu ndipo wakhutitsa wanjala ndi zinthu zabwino.
[10] Ena anakhala mu mdima ndi mʼchisoni chachikulu, amʼndende ovutika mʼmaunyolo achitsulo,
[11] pakuti iwowo anawukira mawu a Mulungu ndi kunyoza uphungu wa Wammwambamwamba.
[12] Kotero Iye anawapereka kuti agwire ntchito yakalavulagaga; anagwa pansi ndipo panalibe woti awathandize.
[13] Pamenepo analirira Yehova mʼmasautso awo ndipo Iye anawapulumutsa ku masautso awo.
[14] Yehova anawatulutsa mu mdima ndi mʼchisoni chachikulu ndipo anadula maunyolo awo.
[15] Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosatha ndi machitidwe ake odabwitsa kwa anthu onse,
[16] pakuti Iye amathyola zipata zamkuwa ndi kudula pakati mipiringidzo yachitsulo.
[17] Ena anakhala zitsiru chifukwa cha njira zawo zowukira, ndipo anamva zowawa chifukwa cha mphulupulu zawo.
[18] Iwo ananyansidwa ndi chakudya chilichonse ndipo anafika pafupi ndi zipata za imfa.
[19] Pamenepo analirira Yehova mʼmasautso awo ndipo Iye anawapulumutsa ku masautso awowo.
[20] Iye anatumiza mawu ake ndi kuwachiritsa; anawalanditsa ku manda.
[21] Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosatha ndi machitidwe ake odabwitsa kwa anthu.
[22] Apereke nsembe yachiyamiko ndi kufotokoza za ntchito zake ndi nyimbo zachimwemwe.
[23] Ena anayenda pa nyanja mʼsitima zapamadzi; Iwo anali anthu amalonda pa nyanja yayikulu.
[24] Anaona ntchito za Yehova, machitidwe ake odabwitsa mʼnyanja yakuya.
[25] Pakuti Iye anayankhula ndi kuwutsa mphepo yamkuntho imene inabweretsa mafunde ataliatali.
[26] Sitima za pamadzizo zinatukulidwa mmwamba ndi kutsikira pansi pakuya; pamene amawonongeka, kulimba mtima kwawo kunasungunuka.
[27] Anachita chizungulire ndi kudzandira ngati anthu oledzera; anali pa mapeto a moyo wawo.
[28] Pamenepo analirira Yehova mʼmasautso awo ndipo Iyeyo anawapulumutsa ku masautso awo.
[29] Yehova analetsa namondwe, mafunde a mʼnyanja anatontholetsedwa.
[30] Anali osangalala pamene kunakhala bata, ndipo Iye anawatsogolera ku dooko limene amalifuna.
[31] Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosatha ndi machitidwe ake odabwitsa kwa anthu.
[32] Akuze Iye mu msonkhano wa anthu ndi kumutamanda pabwalo la akuluakulu.
[33] Iye anasandutsa mitsinje kukhala chipululu, akasupe otuluka madzi kukhala nthaka yowuma,
[34] ndiponso nthaka yachonde kukhala nthaka yamchere, chifukwa cha kuyipa kwa amene amakhala kumeneko.
[35] Anasandutsa chipululu kukhala mayiwe a madzi ndi nthaka yowuma kukhala akasupe a madzi oyenda;
[36] kumeneko Iye anabweretsa anthu anjala kuti azikhalako, ndipo iwo anamanga mzinda woti akhazikikeko.
[37] Anafesa mbewu mʼminda ndi kudzala mipesa ndipo anakolola zipatso zochuluka;
[38] Yehova anawadalitsa, ndipo chiwerengero chawo chinachuluka kwambiri, ndipo Iye sanalole kuti ziweto zawo zithe.
[39] Kenaka chiwerengero chawo chinachepa ndipo iwo anatsitsidwa chifukwa cha mazunzo, mavuto ndi chisoni;
[40] Iye amene amakhuthulira mʼnyozo pa olemekezeka anawachititsa kuyendayenda mʼmalo owumawo wopanda njira.
[41] Koma Iyeyo anakweza anthu osowa kuchoka ku masautso awo ngati magulu a nkhosa.
[42] Anthu olungama mtima amaona ndi kusangalala, koma anthu onse oyipa amatseka pakamwa pawo.
[43] Aliyense wanzeru asamalitse zinthu zimenezi ndi kuganizira za chikondi chachikulu cha Yehova.